< Masalimo 49 >
1 Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la ana a Kora. Imvani izi anthu a mitundu yonse; mvetserani, nonse amene mumakhala pa dziko lonse,
2 anthu wamba pamodzi ndi anthu odziwika, olemera pamodzinso ndi osauka:
3 Pakamwa panga padzayankhula mawu anzeru; mawu ochokera mu mtima mwanga adzapereka nzeru.
4 Ndidzatchera khutu langa ku mwambo, ndi pangwe ndidzafotokoza momveka mwambi wanga.
5 Ine ndichitirenji mantha pamene masiku oyipa afika, pamene achinyengo oyipa andizungulira.
6 Iwo amene adalira kulemera kwawo ndi kutamandira kuchuluka kwa chuma chawo?
7 Palibe munthu amene angawombole moyo wa mnzake kapena kuperekera mnzake dipo kwa Mulungu.
8 Dipo la moyo ndi la mtengowapatali, palibe malipiro amene angakwanire,
9 kuti iye akhale ndi moyo mpaka muyaya ndi kusapita ku manda.
10 Pakuti onse amaona kuti anthu anzeru amamwalira; opusa ndi opanda nzeru chimodzimodzinso amawonongeka ndipo amasiyira chuma chawo anthu ena.
11 Manda awo adzakhala nyumba zawo mpaka muyaya, malo awo okhalako kwa nthawi yonse ya mibado yawo, ngakhale anatchula malo mayina awo.
12 Ngakhale munthu akhale wachuma chotani, adzafa ngati nyama.
13 Izi ndi zimene zimachitikira iwo amene amadzidalira okha, ndi owatsatira awo amene amavomereza zimene amayankhula. (Sela)
14 Monga nkhosa iwo ayenera kupita ku manda, ndipo imfa idzawadya. Olungama adzawalamulira mmawa; matupi awo adzavunda mʼmanda, kutali ndi nyumba zawo zaufumu. (Sheol )
15 Koma Mulungu adzawombola moyo wanga kuchoka ku manda; ndithu Iye adzanditengera kwa Iye mwini. (Sheol )
16 Usavutike mu mtima pamene munthu akulemera, pamene ulemerero wa nyumba yake ukuchulukirachulukira;
17 Pakuti sadzatenga kanthu pamodzi naye pamene wamwalira, ulemerero wake sudzapita pamodzi naye.
18 Ngakhale pamene munthuyo ali moyo amadziyesa wodala, ndipo ngakhale atamandidwe pamene zinthu zikumuyendera bwino,
19 iyeyo adzakakhala pamodzi ndi mʼbado wa makolo ake, amene sadzaonanso kuwala.
20 Munthu amene ali ndi chuma koma wopanda nzeru adzafa ngati nyama yakuthengo.