< Masalimo 48 >

1 Nyimbo. Salimo la ana a Kora. Wamkulu ndi Yehova, ndi woyenera kwambiri matamando mu mzinda wa Mulungu wathu, phiri lake loyera.
Psalmus, Laus Cantici filiis Core secunda sabbati. Magnus Dominus, et laudabilis nimis in civitate Dei nostri, in monte sancto eius.
2 Lokongola mu utali mwake, chimwemwe cha dziko lonse lapansi. Malo aatali kwambiri a Zafoni ndiye Phiri la Ziyoni, mzinda wa Mfumu yayikulu.
Fundatur exultatione universae terrae mons Sion, latera Aquilonis, civitas Regis magni.
3 Mulungu ali mu malinga ake; Iye wadzionetsa yekha kuti ndiye malinga akewo.
Deus in domibus eius cognoscetur, cum suscipiet eam.
4 Pamene mafumu anasonkhana pamodzi, pamene anayendera pamodzi kudzalimbana nafe,
Quoniam ecce reges terrae congregati sunt: convenerunt in unum.
5 iwo anaona mzindawo ndipo anadabwa kwambiri; anathawa ndi mantha aakulu.
Ipsi videntes sic admirati sunt, conturbati sunt, commoti sunt:
6 Pomwepo anagwidwa nako kunjenjemera, ululu wonga wa mkazi woyembekezera pa nthawi yochira.
tremor apprehendit eos. Ibi dolores ut parturientis,
7 Inu munawawononga monga sitima zapamadzi za ku Tarisisi zitawonongeka ndi mphepo ya kummawa.
in spiritu vehementi conteres naves Tharsis.
8 Monga momwe tinamvera, kotero ife tinaona mu mzinda wa Yehova Wamphamvuzonse, mu mzinda wa Mulungu wathu. Mulungu adzawuteteza kwamuyaya.
Sicut audivimus, sic vidimus in civitate Domini virtutum, in civitate Dei nostri: Deus fundavit eam in aeternum.
9 Mʼkati mwa Nyumba yanu Mulungu, ife timalingaliramo zachikondi chanu chosasinthika.
Suscepimus Deus misericordiam tuam, in medio templi tui.
10 Monga dzina lanu, Inu Mulungu, matamando anu amafika ku malekezero a dziko lapansi dzanja lanu lamanja ladzaza ndi chilungamo.
Secundum nomen tuum Deus, sic et laus tua in fines terrae: iustitia plena est dextera tua.
11 Phiri la Ziyoni likukondwera, midzi ya Yuda ndi yosangalala chifukwa cha maweruzo anu.
Laetetur mons Sion, et exultent filiae Iudae, propter iudicia tua Domine.
12 Yendayendani mu Ziyoni, uzungulireni mzindawo, werengani nsanja zake.
Circumdate Sion, et complectimini eam: narrate in turribus eius.
13 Yangʼanitsitsani bwino mipanda yake, penyetsetsani malinga ake, kuti mudzafotokoze za izo ku mʼbado wotsatira.
Ponite corda vestra in virtute eius: et distribuite domos eius, ut enarretis in progenie altera.
14 Pakuti Mulungu uyu ndi Mulungu wathu ku nthawi zosatha; Iye adzakhala mtsogoleri wathu mpaka ku mapeto.
Quoniam hic est Deus, Deus noster in aeternum, et in saeculum saeculi: ipse reget nos in saecula.

< Masalimo 48 >