< Masalimo 47 >

1 Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la ana a Kora. Ombani mʼmanja, inu anthu onse; fuwulani kwa Mulungu ndi mawu achimwemwe.
To the chief Musician. Of the sons of Korah. A Psalm. All ye peoples, clap your hands; shout unto God with the voice of triumph!
2 Ndi woopsadi Yehova Wammwambamwamba; Mfumu yayikulu ya dziko lonse lapansi!
For Jehovah, the Most High, is terrible, a great king over all the earth.
3 Iye anatigonjetsera mitundu yambirimbiri ya anthu; anayika anthu pansi pa mapazi athu.
He subdueth the peoples under us, and the nations under our feet.
4 Iye anatisankhira cholowa chathu, chonyaditsa cha Yakobo, amene anamukonda. (Sela)
He hath chosen our inheritance for us, the excellency of Jacob whom he loved. (Selah)
5 Mulungu wakwera, anthu akumufuwulira mwachimwemwe, Yehova wakwera, akumuyimbira malipenga.
God is gone up amid shouting, Jehovah amid the sound of the trumpet.
6 Imbani matamando kwa Mulungu, imbani matamando; imbani matamando kwa mfumu yathu, imbani matamando.
Sing psalms of God, sing psalms; sing psalms unto our King, sing psalms!
7 Pakuti Mulungu ndi mfumu ya dziko lonse lapansi; imbirani Iye salimo la matamando.
For God is the King of all the earth; sing psalms with understanding.
8 Mulungu akulamulira mitundu ya anthu; Mulungu wakhala pa mpando wake waufumu woyera.
God reigneth over the nations; God sitteth upon the throne of his holiness.
9 Anthu otchuka mwa anthu a mitundu ina asonkhana monga anthu a Mulungu wa Abrahamu, pakuti mafumu a dziko lapansi ndi ake a Mulungu; Iye wakwezedwa kwakukulu.
The willing-hearted of the peoples have gathered together, [with] the people of the God of Abraham. For unto God [belong] the shields of the earth: he is greatly exalted.

< Masalimo 47 >