< Masalimo 46 >

1 Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Ndakatulo ya ana a Kora. Nyimbo ya anamwali. Mulungu ndiye kothawira kwathu ndi mphamvu yathu, thandizo lopezekeratu pa nthawi ya mavuto.
To the chief Musician for the sons of Korah, A Song upon Alamoth. God is our refuge and strength, a very present help in trouble.
2 Nʼchifukwa chake sitidzaopa ngakhale dziko lapansi lisunthike, ngakhale mapiri agwe pakati pa nyanja,
Therefore will we not fear, though the earth shall be removed, and though the mountains shall be carried into the midst of the sea;
3 ngakhale madzi ake atakokoma ndi kuchita thovu, ngakhale mapiri agwedezeke ndi kukokoma kwake.
Though its waters shall roar and be troubled, though the mountains shake with its swelling. (Selah)
4 Kuli mtsinje umene njira zake za madzi zimasangalatsa mzinda wa Mulungu, malo oyera kumene Wammwambamwamba amakhalako.
There is a river, the streams of which shall make glad the city of God, the holy place of the tabernacles of the most High.
5 Mulungu ali mʼkati mwake, iwo sudzagwa; Mulungu adzawuthandiza mmawa.
God is in the midst of her; she shall not be moved: God shall help her, and that right early.
6 Mitundu ikupokosera, mafumu akugwa; Iye wakweza mawu ake, dziko lapansi likusungunuka.
The heathen raged, the kingdoms were moved: he uttered his voice, the earth melted.
7 Yehova Wamphamvuzonse ali ndi ife, Mulungu wa Yakobo ndi linga lathu.
The LORD of hosts is with us; the God of Jacob is our refuge. (Selah)
8 Bwerani kuti mudzaone ntchito za Yehova, chiwonongeko chimene wachibweretsa pa dziko lapansi.
Come, behold the works of the LORD, what desolations he hath made in the earth.
9 Iye amathetsa nkhondo ku malekezero a dziko lapansi; Iye amathyola uta ndi kupindapinda mkondo; amatentha zishango ndi moto.
He maketh wars to cease to the end of the earth; he breaketh the bow, and cutteth the spear asunder; he burneth the chariot in the fire.
10 Iye akuti, “Khala chete, ndipo dziwa kuti ndine Mulungu; ndidzakwezedwa pakati pa mitundu ya anthu; ine ndidzakwezedwa mʼdziko lapansi.”
Be still, and know that I am God: I will be exalted among the heathen, I will be exalted in the earth.
11 Yehova Wamphamvuzonse ali ndi ife, Mulungu wa Yakobo ndi linga lathu.
The LORD of hosts is with us; the God of Jacob is our refuge. (Selah)

< Masalimo 46 >