< Masalimo 45 >

1 Kwa mtsogoleri wamayimbidwe. Monga mwa mayimbidwe a “Maluwa a Kakombo.” Salimo la ana a Kora. Nyimbo ya pa ukwati. Mtima wanga watakasika ndi nkhani yokoma pamene ndikulakatula mawu anga kwa mfumu; lilime langa ndi cholembera cha wolemba waluso.
למנצח על-ששנים לבני-קרח משכיל שיר ידידת ב רחש לבי דבר טוב-- אמר אני מעשי למלך לשוני עט סופר מהיר
2 Inu ndinu abwino kwambiri kuposa anthu onse ndipo milomo yanu inadzozedwa ndi chikondi cha Mulungu chosasinthika, popeza Mulungu wakudalitsani kwamuyaya.
יפיפית מבני אדם-- הוצק חן בשפתותיך על-כן ברכך אלהים לעולם
3 Mangirirani lupanga lanu mʼchiwuno mwanu, inu munthu wamphamvu; mudziveke nokha ndi ulemerero ndi ukulu wanu.
חגור-חרבך על-ירך גבור-- הודך והדרך
4 Mu ukulu wanu mupite mutakwera mwachigonjetso mʼmalo mwa choonadi, kudzichepetsa ndi chilungamo; dzanja lanu lamanja lionetsere ntchito zanu zoopsa.
והדרך צלח רכב-- על-דבר-אמת וענוה-צדק ותורך נוראות ימינך
5 Mivi yanu yakuthwa ilase mitima ya adani a mfumu, mitundu ya anthu igwe pansi pa mapazi anu.
חציך שנונים עמים תחתיך יפלו בלב אויבי המלך
6 Mpando wanu waufumu, Inu Mulungu, udzakhala ku nthawi za nthawi; ndodo yaufumu yachilungamo idzakhala ndodo yaufumu ya ufumu wanu.
כסאך אלהים עולם ועד שבט מישר שבט מלכותך
7 Inu mumakonda chilungamo ndi kudana ndi zoyipa; choncho Mulungu, Mulungu wanu, wakukhazikani pamwamba pa anzanu pokudzozani ndi mafuta a chimwemwe.
אהבת צדק ותשנא-רשע על-כן משחך אלהים אלהיך שמן ששון-- מחברך
8 Mikanjo yanu yonse ndi yonunkhira ndi mure ndi aloe ndi kasiya; kuchokera ku nyumba zaufumu zokongoletsedwa ndi mnyanga wanjovu nyimbo za zoyimbira zazingwe zimakusangalatsani.
מר-ואהלות קציעות כל-בגדתיך מן-היכלי שן מני שמחוך
9 Ana aakazi a mafumu ali pakati pa akazi anu olemekezeka; ku dzanja lanu lamanja kuli mkwatibwi waufumu ali mu golide wa ku Ofiri.
בנות מלכים ביקרותיך נצבה שגל לימינך בכתם אופיר
10 Tamvera, iwe mwana wa mkazi ganizira ndipo tchera khutu; iwala anthu ako ndi nyumba ya abambo ako.
שמעי-בת וראי והטי אזנך ושכחי עמך ובית אביך
11 Mfumu yathedwa nzeru chifukwa cha kukongola kwako; mulemekeze pakuti iyeyo ndiye mbuye wako.
ויתאו המלך יפיך כי-הוא אדניך והשתחוי-לו
12 Mwana wa mkazi wa ku Turo adzabwera ndi mphatso, amuna a chuma adzafunafuna kukoma mtima kwako.
ובת-צר במנחה פניך יחלו--עשירי עם
13 Wokongola kwambiri ndi mwana wa mfumu ali mʼchipinda mwake, chovala chake ndi cholukidwa ndi thonje ndi golide.
כל-כבודה בת-מלך פנימה ממשבצות זהב לבושה
14 Atavala zovala zamaluwamaluwa akupita naye kwa mfumu; anamwali okhala naye akumutsatira ndipo abweretsedwa kwa inu.
לרקמות תובל למלך בתולות אחריה רעותיה--מובאות לך
15 Iwo akuwaperekeza ndi chimwemwe ndi chisangalalo; akulowa mʼnyumba yaufumu.
תובלנה בשמחת וגיל תבאינה בהיכל מלך
16 Ana ako aamuna adzatenga malo a makolo ako; udzachititsa kuti akhale ana a mfumu mʼdziko lonse.
תחת אבתיך יהיו בניך תשיתמו לשרים בכל-הארץ
17 Ndidzabukitsa mbiri yako mʼmibado yonse; choncho mitundu yonse idzakutamanda ku nthawi za nthawi.
אזכירה שמך בכל-דר ודר על-כן עמים יהודוך לעלם ועד

< Masalimo 45 >