< Masalimo 44 >

1 Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Ndakatulo ya ana a Kora. Ife tamva ndi makutu athu, Inu Mulungu; makolo athu atiwuza zimene munachita mʼmasiku awo, masiku akalekalewo.
לַמְנַצֵּחַ לִבְנֵי־קֹרַח מַשְׂכִּֽיל׃ אֱלֹהִים ׀ בְּאָזְנֵינוּ שָׁמַעְנוּ אֲבוֹתֵינוּ סִפְּרוּ־לָנוּ פֹּעַל פָּעַלְתָּ בִֽימֵיהֶם בִּימֵי קֶֽדֶם׃
2 Ndi dzanja lanu munathamangitsa mitundu ya anthu ena ndi kudzala makolo athu; Inu munakantha mitundu ya anthu, koma makolo athuwo Inu munawapatsa ufulu.
אַתָּה ׀ יָדְךָ גּוֹיִם הוֹרַשְׁתָּ וַתִּטָּעֵם תָּרַע לְאֻמִּים וַֽתְּשַׁלְּחֵֽם׃
3 Sanalande dziko ndi lupanga lawo, si mkono wawo umene unawabweretsera chigonjetso, koma ndi dzanja lanu lamanja, mkono wanu ndi kuwala kwa nkhope yanu, pakuti munawakonda.
כִּי לֹא בְחַרְבָּם יָרְשׁוּ אָרֶץ וּזְרוֹעָם לֹא־הוֹשִׁיעָה לָּמוֹ כִּֽי־יְמִֽינְךָ וּזְרוֹעֲךָ וְאוֹר פָּנֶיךָ כִּי רְצִיתָֽם׃
4 Inu ndinu Mfumu yanga ndi Mulungu wanga amene mumalamulira chigonjetso cha Yakobo.
אַתָּה־הוּא מַלְכִּי אֱלֹהִים צַוֵּה יְשׁוּעוֹת יַעֲקֹֽב׃
5 Kudzera kwa inu ife timabweza adani athu; kudzera mʼdzina lanu timapondereza otiwukirawo.
בְּךָ צָרֵינוּ נְנַגֵּחַ בְּשִׁמְךָ נָבוּס קָמֵֽינוּ׃
6 Sindidalira uta wanga, lupanga langa silindibweretsera chigonjetso;
כִּי לֹא בְקַשְׁתִּי אֶבְטָח וְחַרְבִּי לֹא תוֹשִׁיעֵֽנִי׃
7 koma Inu mumatigonjetsera adani athu, mumachititsa manyazi amene amadana nafe.
כִּי הוֹשַׁעְתָּנוּ מִצָּרֵינוּ וּמְשַׂנְאֵינוּ הֱבִישֽׁוֹתָ׃
8 Timanyadira mwa Mulungu wathu tsiku lonse, ndipo tidzatamanda dzina lanu kwamuyaya.
בֵּֽאלֹהִים הִלַּלְנוּ כָל־הַיּוֹם וְשִׁמְךָ ׀ לְעוֹלָם נוֹדֶה סֶֽלָה׃
9 Koma tsopano mwatikana ndi kutichepetsa; Inu simupitanso ndi ankhondo athu.
אַף־זָנַחְתָּ וַתַּכְלִימֵנוּ וְלֹא־תֵצֵא בְּצִבְאוֹתֵֽינוּ׃
10 Munachititsa ife kubwerera mʼmbuyo pamaso pa mdani ndipo amene amadana nafe atilanda katundu.
תְּשִׁיבֵנוּ אָחוֹר מִנִּי־צָר וּמְשַׂנְאֵינוּ שָׁסוּ לָֽמוֹ׃
11 Inu munatipereka kuti tiwonongedwe monga nkhosa ndipo mwatibalalitsa pakati pa anthu a mitundu ina.
תִּתְּנֵנוּ כְּצֹאן מַאֲכָל וּבַגּוֹיִם זֵרִיתָֽנוּ׃
12 Inu munagulitsa anthu anu pa mtengo wotsika, osapindulapo kanthu pa malondawo.
תִּמְכֹּֽר־עַמְּךָ בְלֹא־הוֹן וְלֹא־רִבִּיתָ בִּמְחִירֵיהֶֽם׃
13 Mwachititsa kuti tikhale chochititsa manyazi kwa anthu a mitundu ina, chonyozeka ndi chothetsa nzeru kwa iwo amene atizungulira.
תְּשִׂימֵנוּ חֶרְפָּה לִשְׁכֵנֵינוּ לַעַג וָקֶלֶס לִסְבִיבוֹתֵֽינוּ׃
14 Mwachititsa kuti tikhale onyozeka pakati pa anthu a mitundu ina; anthu amapukusa mitu yawo akationa.
תְּשִׂימֵנוּ מָשָׁל בַּגּוֹיִם מְנֽוֹד־רֹאשׁ בַּל־אֻמִּֽים׃
15 Manyazi anga ali pamaso panga tsiku lonse ndipo nkhope yanga yaphimbidwa ndi manyazi
כָּל־הַיּוֹם כְּלִמָּתִי נֶגְדִּי וּבֹשֶׁת פָּנַי כִּסָּֽתְנִי׃
16 chifukwa cha mawu otonza a iwo amene amandinyoza ndi kundichita chipongwe, chifukwa cha mdani amene watsimikiza kubwezera.
מִקּוֹל מְחָרֵף וּמְגַדֵּף מִפְּנֵי אוֹיֵב וּמִתְנַקֵּֽם׃
17 Zonsezi zinatichitikira ngakhale kuti ifeyo sitinayiwale Inu kapena kuonetsa kusakhulupirika pa pangano lanu.
כָּל־זֹאת בָּאַתְנוּ וְלֹא שְׁכַחֲנוּךָ וְלֹֽא־שִׁקַּרְנוּ בִּבְרִיתֶֽךָ׃
18 Mitima yathu sinabwerere mʼmbuyo; mapazi athu sanatayike pa njira yanu.
לֹא־נָסוֹג אָחוֹר לִבֵּנוּ וַתֵּט אֲשֻׁרֵינוּ מִנִּי אָרְחֶֽךָ׃
19 Koma Inu mwatiphwanya ndi kuchititsa kuti tikhale ozunzidwa ndi ankhandwe ndipo mwatiphimba ndi mdima waukulu.
כִּי דִכִּיתָנוּ בִּמְקוֹם תַּנִּים וַתְּכַס עָלֵינוּ בְצַלְמָֽוֶת׃
20 Tikanayiwala dzina la Mulungu wathu kapena kutambasulira manja athu kwa mulungu wachilendo,
אִם־שָׁכַחְנוּ שֵׁם אֱלֹהֵינוּ וַנִּפְרֹשׂ כַּפֵּינוּ לְאֵל זָֽר׃
21 kodi Mulungu wathu sakanazidziwa zimenezi, pakuti Iye amadziwa zinsinsi zamumtima?
הֲלֹא אֱלֹהִים יַֽחֲקָר־זֹאת כִּֽי־הוּא יֹדֵעַ תַּעֲלֻמוֹת לֵֽב׃
22 Komabe chifukwa cha Inu timakumana ndi imfa tsiku lonse, tili ngati nkhosa zoyenera kuti ziphedwe.
כִּֽי־עָלֶיךָ הֹרַגְנוּ כָל־הַיּוֹם נֶחְשַׁבְנוּ כְּצֹאן טִבְחָֽה׃
23 Dzukani Ambuye! Nʼchifukwa chiyani mukugona! Dziwutseni nokha! Musatikane kwamuyaya.
עוּרָה ׀ לָמָּה תִישַׁן ׀ אֲדֹנָי הָקִיצָה אַל־תִּזְנַח לָנֶֽצַח׃
24 Nʼchifukwa chiyani mukubisa nkhope yanu, ndi kuyiwala mavuto athu ndi kuponderezedwa kwathu?
לָֽמָּה־פָנֶיךָ תַסְתִּיר תִּשְׁכַּח עָנְיֵנוּ וְֽלַחֲצֵֽנוּ׃
25 Tatsitsidwa pansi mpaka pa fumbi; matupi athu amatirira pa dothi.
כִּי שָׁחָה לֶעָפָר נַפְשֵׁנוּ דָּבְקָה לָאָרֶץ בִּטְנֵֽנוּ׃
26 Imirirani ndi kutithandiza, tiwomboleni chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika.
קוּמָֽה עֶזְרָתָה לָּנוּ וּפְדֵנוּ לְמַעַן חַסְדֶּֽךָ׃

< Masalimo 44 >