< Masalimo 43 >
1 Onetsani kusalakwa kwanga Inu Mulungu; ndipo mundinenere mlandu wanga kutsutsana ndi mtundu wosapembedza; mundilanditse mʼmanja mwa achinyengo ndi anthu oyipa.
Judge me, O God, and plead my cause against a profane nation. O deliver me from the deceitful and unjust man.
2 Pajatu Inu Mulungu ndinu mphamvu zanga. Nʼchifukwa chiyani mwandikana ine? Nʼchifukwa chiyani ndiyenera kuyenda ndikulira, woponderezedwa ndi mdani?
For thou are the God of my strength. Why have thou cast me off? Why do I go mourning because of the oppression of the enemy?
3 Tumizani kuwunika kwanu ndi choonadi chanu kuti zinditsogolere; mulole kuti zindifikitse ku phiri lanu loyera, kumalo kumene inu mumakhala.
O send out thy light and thy truth. Let them lead me. Let them bring me to thy holy hill, and to thy tabernacles.
4 Ndipo ndidzapita ku guwa lansembe la Mulungu, kwa Mulungu, chimwemwe changa ndi chikondwerero changa. Ndidzakutamandani ndi zeze, Inu Mulungu wanga.
Then I will go to the altar of God, to God my exceeding joy, and I will praise thee upon the harp, O God, my God.
5 Nʼchifukwa chiyani uli ndi chisoni iwe moyo wanga? Nʼchifukwa chiyani wakhumudwa iwe mʼkati mwanga? Khulupirira Mulungu, pakuti ndidzamutamandabe Iye, Mpulumutsi wanga ndi Mulungu wanga.
Why are thou cast down, O my soul? And why are thou disquieted within me? Hope thou in God, for I shall yet praise him, the help of my countenance, and my God.