< Masalimo 42 >
1 Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Ndakatulo ya ana a Kora. Monga mbawala ipuma wefuwefu kufunafuna mitsinje yamadzi, kotero moyo wanga upuma wefuwefu kufunafuna Inu Mulungu.
TO THE OVERSEER. AN INSTRUCTION OF THE SONS OF KORAH. As a deer pants for streams of water, So my soul pants toward You, O God.
2 Moyo wanga uli ndi ludzu lofuna Mulungu, lofuna Mulungu wamoyo. Kodi ndipite liti kukakumana ndi Mulungu?
My soul thirsted for God, for the living God, When do I enter and see the face of God?
3 Misozi yanga yakhala chakudya changa usana ndi usiku, pamene anthu akunena kwa ine tsiku lonse kuti, “Mulungu wako ali kuti?”
My tear has been bread day and night to me, In their saying to me all the day, “Where [is] your God?”
4 Zinthu izi ndimazikumbukira pamene ndikukhuthula moyo wanga: momwe ndinkapitira ndi gulu lalikulu, kutsogolera mayendedwe a ku Nyumba ya Mulungu ndi mfuwu yachimwemwe ndi mayamiko pakati pa anthu a pa chikondwerero.
These I remember, and pour out my soul in me, For I pass over into the shelter, I go softly with them to the house of God, With the voice of singing and confession, The multitude keeping celebration!
5 Nʼchifukwa chiyani uli ndi chisoni, iwe moyo wanga? Nʼchifukwa chiyani wakhumudwa iwe mʼkati mwanga? Yembekezera Mulungu, pakuti ndidzamulambirabe, Mpulumutsi wanga ndi
Why bow yourself, O my soul? Indeed, are you troubled within me? Wait for God, for I still confess Him: The salvation of my countenance—my God!
6 Mulungu wanga. Moyo wanga uli ndi chisoni mʼkati mwanga kotero ndidzakumbukira Inu kuchokera ku dziko la Yorodani, ku mitunda ya Herimoni kuchokera ku phiri la Mizara.
My soul bows itself in me, Therefore I remember You from the land of Jordan, And of the Hermons, from Mount Mizar.
7 Madzi akuya akuyitana madzi akuya mu mkokomo wa mathithi anu; mafunde anu onse obwera mwamphamvu andimiza.
Deep is calling to deep At the noise of Your waterspouts, All Your breakers and Your billows passed over me.
8 Koma usana Yehova amalamulira chikondi chake, nthawi ya usiku nyimbo yake ili nane; pemphero kwa Mulungu wa moyo wanga.
By day YHWH commands His kindness, And by night a song [is] with me, A prayer to the God of my life.
9 Ine ndikuti kwa Mulungu Thanthwe langa, “Nʼchifukwa chiyani mwandiyiwala? Nʼchifukwa chiyani ndiyenera kuyenda ndikulira, woponderezedwa ndi mdani?”
I say to God my Rock, “Why have You forgotten me? Why do I go mourning in the oppression of an enemy?”
10 Mafupa anga ali ndi ululu wakufa nawo pamene adani anga akundinyoza, tsiku lonse akunena kuti, “Mulungu wako ali kuti?”
With a sword in my bones My adversaries have reproached me, In their saying to me all the day, “Where [is] your God?”
11 Bwanji ukumva chisoni, iwe mtima wanga? Chifukwa chiyani ukuvutika chonchi mʼkati mwanga? Khulupirira Mulungu, pakuti ndidzamutamandanso, Iye amene ali thandizo langa ndi Mulungu wanga.
Why bow yourself, O my soul? And why are you troubled within me? Wait for God, for I still confess Him, The salvation of my countenance, and my God!