< Masalimo 40 >
1 Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Mofatsa ndinadikira Yehova Iye anatembenukira kwa ine ndipo anamva kulira kwanga.
大卫的诗,交与伶长。 我曾耐性等候耶和华; 他垂听我的呼求。
2 Ananditulutsa mʼdzenje lachitayiko, mʼthope ndi mʼchithaphwi; Iye anakhazikitsa mapazi anga pa thanthwe ndipo anandipatsa malo oyimapo olimba.
他从祸坑里, 从淤泥中,把我拉上来, 使我的脚立在磐石上, 使我脚步稳当。
3 Iye anayika nyimbo yatsopano mʼkamwa mwanga, nyimbo yamatamando kwa Mulungu wanga. Ambiri adzaona, nadzaopa ndipo adzakhulupirira Yehova.
他使我口唱新歌, 就是赞美我们 神的话。 许多人必看见而惧怕, 并要倚靠耶和华。
4 Ndi wodala munthu amakhulupirira Yehova; amene sayembekezera kwa odzikuza, kapena kwa amene amatembenukira kwa milungu yabodza.
那倚靠耶和华、 不理会狂傲和偏向虚假之辈的, 这人便为有福!
5 Zambiri, Yehova Mulungu wanga, ndi zodabwitsa zimene Inu mwachita. Zinthu zimene munazikonzera ife palibe amene angathe kukuwerengerani. Nditati ndiyankhule ndi kufotokozera, zidzakhala zambiri kuzifotokoza.
耶和华—我的 神啊,你所行的奇事, 并你向我们所怀的意念甚多,不能向你陈明; 若要陈明,其事不可胜数。
6 Nsembe ndi zopereka Inu simuzifuna, koma makutu anga mwawatsekula; zopereka zopsereza ndi zopereka chifukwa cha tchimo Inu simunazipemphe.
祭物和礼物,你不喜悦; 你已经开通我的耳朵。 燔祭和赎罪祭非你所要。
7 Kotero ndinati, “Ndili pano, ndabwera. Mʼbuku mwalembedwa za ine.
那时我说:看哪,我来了! 我的事在经卷上已经记载了。
8 Ndikufuna kuchita chifuniro chanu, Inu Mulungu wanga; lamulo lanu lili mu mtima mwanga.”
我的 神啊,我乐意照你的旨意行; 你的律法在我心里。
9 Ndikulalikira uthenga wa chilungamo chanu mu msonkhano waukulu; sinditseka milomo yanga monga mukudziwa Inu Yehova.
我在大会中宣传公义的佳音; 我必不止住我的嘴唇。 耶和华啊,这是你所知道的。
10 Sindibisa chilungamo chanu mu mtima mwanga; ndinayankhula za kukhulupirika kwanu ndi chipulumutso chanu. Ine sindiphimba chikondi chanu ndi choonadi chanu pa msonkhano waukulu.
我未曾把你的公义藏在心里; 我已陈明你的信实和你的救恩; 我在大会中未曾隐瞒你的慈爱和诚实。
11 Musandichotsere chifundo chanu Yehova; chikondi chanu ndi choonadi chanu zinditeteze nthawi zonse.
耶和华啊,求你不要向我止住你的慈悲! 愿你的慈爱和诚实常常保佑我!
12 Pakuti mavuto osawerengeka andizungulira; machimo anga andigonjetsa, ndipo sindingathe kuona. Alipo ambiri kuposa tsitsi la mʼmutu mwanga, ndipo mtima wanga ukufowoka mʼkati mwanga.
因有无数的祸患围困我, 我的罪孽追上了我,使我不能昂首; 这罪孽比我的头发还多, 我就心寒胆战。
13 Pulumutseni Yehova; Bwerani msanga Yehova kudzandithandiza.
耶和华啊,求你开恩搭救我! 耶和华啊,求你速速帮助我!
14 Onse amene akufunafuna kuchotsa moyo wanga achititsidwe manyazi ndi kusokonezedwa; onse amene amakhumba chiwonongeko changa abwezedwe mwamanyazi.
愿那些寻找我、要灭我命的,一同抱愧蒙羞! 愿那些喜悦我受害的,退后受辱!
15 Iwo amene amanena kwa ine kuti, “Hee! Hee!” abwerere akuchita manyazi.
愿那些对我说阿哈、阿哈的, 因羞愧而败亡!
16 Koma iwo amene amafunafuna Inu akondwere ndi kusangalala mwa Inu; iwo amene amakonda chipulumutso chanu nthawi zonse anene kuti, “Yehova akwezeke!”
愿一切寻求你的,因你高兴欢喜! 愿那些喜爱你救恩的,常说:当尊耶和华为大!
17 Komabe Ine ndine wosauka ndi wosowa; Ambuye andiganizire. Inu ndinu thandizo langa ndi wondiwombola wanga; Inu Mulungu wanga, musachedwe.
但我是困苦穷乏的,主仍顾念我; 你是帮助我的,搭救我的。 神啊,求你不要耽延!