< Masalimo 38 >
1 Salimo la Davide. Kupempha. Yehova musandidzudzule mutapsa mtima kapena kundilanga muli ndi ukali.
2 Pakuti mivi yanu yandilasa, ndipo dzanja lanu latsika ndipo landifikira.
3 Chifukwa cha ukali wanu mulibe thanzi mʼthupi langa; mafupa anga alibe mphamvu chifukwa cha tchimo langa.
4 Kulakwa kwanga kwandipsinja ngati katundu wolemera kwambiri kuposa mphamvu zanga.
5 Mabala anga akuwola ndipo akununkha chifukwa cha uchitsiru wa moyo wanga wauchimo.
6 Ine ndapindika msana ndipo ndawerama kwambiri; tsiku lonse ndimangolira.
7 Msana wanga wagwidwa ndi ululu wosasimbika, mulibe thanzi mʼthupi langa.
8 Ndilibe mphamvu ndipo ndakunthidwa kwathunthu; ndikubuwula ndi ululu wa mumtima.
9 Zokhumba zanga zonse zili poonekera pamaso panu Ambuye, kusisima kwanga sikunabisike kwa Inu.
10 Mtima wanga ukugunda, mphamvu zanga zikutha; ngakhale kuwala kwachoka mʼmaso mwanga.
11 Abwenzi anga ndi anzanga akundipewa chifukwa cha mabala anga; anansi anga akhala kutali nane.
12 Iwo amene akufunafuna moyo wanga atchera misampha yawo, oti andipwetekewo amayankhula za kuwonongeka kwanga; tsiku lonse amakonza zachinyengo.
13 Ine ndili ngati munthu wosamva amene sangamve, monga wosayankhula, amene sangathe kutsekula pakamwa pake;
14 Ndakhala ngati munthu amene samva, amene pakamwa pake sipangathe kuyankha.
15 Ndikudikira Inu Yehova; mudzayankha, Inu Ambuye Mulungu wanga.
16 Pakuti Ine ndinati, “Musawalole kuti akondwere kapena kudzikweza okha pa ine pamene phazi langa laterereka.”
17 Pakuti ndili pafupi kugwa, ndipo ndikumva kuwawa nthawi zonse.
18 Ndikuvomereza mphulupulu zanga; ndipo ndavutika ndi tchimo langa.
19 Ambiri ndi adani anga amphamvu; amene amandida popanda chifukwa alipo ochuluka kwambiri.
20 Iwo amene amandibwezera zoyipa mʼmalo mwa zabwino amandinyoza pamene nditsatira zabwino.
21 Inu Yehova, musanditaye; musakhale kutali ndi ine Mulungu wanga.
22 Bwerani msanga kudzandithandiza, Inu Ambuye Mpulumutsi wanga.