< Masalimo 36 >

1 Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide, mtumiki wa Yehova. Uthenga uli mu mtima mwanga wonena za kuchimwa kwa munthu woyipa: Mu mtima mwake mulibe kuopa Mulungu.
למנצח לעבד-יהוה לדוד ב נאם-פשע לרשע בקרב לבי אין-פחד אלהים לנגד עיניו
2 Pakuti iye mʼkuona kwake amadzinyenga yekha kwambiri, sazindikira kapena kudana ndi tchimo lake.
כי-החליק אליו בעיניו למצא עונו לשנא
3 Mawu a pakamwa pake ndi oyipa ndi achinyengo; iyeyo waleka kukhala wanzeru ndi kuchita zabwino.
דברי-פיו און ומרמה חדל להשכיל להיטיב
4 Ngakhale ali pa bedi pake amakonzekera zoyipa; iye amadzipereka yekha ku njira ya uchimo ndipo sakana cholakwa chilichonse.
און יחשב--על-משכבו יתיצב על-דרך לא-טוב רע לא ימאס
5 Chikondi chanu Yehova, chimafika ku mayiko a kumwamba, kukhulupirika kwanu mpaka ku mitambo.
יהוה בהשמים חסדך אמונתך עד-שחקים
6 Chilungamo chanu Mulungu chili ngati mapiri aakulu, chiweruzo chanu chili ngati kuzama kwakukulu. Yehova mumasunga munthu pamodzi ndi chinyama.
צדקתך כהררי-אל--משפטיך תהום רבה אדם ובהמה תושיע יהוה
7 Chikondi chanu chosatha ndi chamtengowapatali! Otchuka pamodzi ndi anthu wamba pakati pa anthu amapeza pothawirapo mu mthunzi wa mapiko anu.
מה-יקר חסדך אלהים ובני אדם--בצל כנפיך יחסיון
8 Iwo amadyerera zinthu zambiri za mʼnyumba yanu; Inu mumawapatsa chakumwa kuchokera mu mtsinje wanu wachikondwerero.
ירוין מדשן ביתך ונחל עדניך תשקם
9 Pakuti kwa Inu kuli kasupe wamoyo; mʼkuwala kwanu ifenso timaona kuwala.
כי-עמך מקור חיים באורך נראה-אור
10 Pitirizani chikondi chanu pa iwo amene amakudziwani, chilungamo chanu kwa olungama mtima.
משך חסדך לידעיך וצדקתך לישרי-לב
11 Musalole kuti phazi la wodzikuza libwere kulimbana nane, kapena dzanja la oyipa kundithamangitsa.
אל-תבואני רגל גאוה ויד-רשעים אל-תנדני
12 Onani momwe ochita zoyipa agonera atagwa, aponyeni pansi, kuti asathe kudzukanso!
שם נפלו פעלי און דחו ולא-יכלו קום

< Masalimo 36 >