< Masalimo 35 >
1 Salimo la Davide. Inu Yehova, mulimbane nawo amene akulimbana nane; mumenyane nawo amene akumenyana nane.
Ipsi David. Iudica Domine nocentes me, expugna impugnantes me.
2 Tengani chishango ndi lihawo; dzukani ndipo bwerani mundithandize.
Apprehende arma et scutum: et exurge in adiutorium mihi.
3 Tengani mkondo ndi nthungo, kulimbana ndi iwo amene akundithamangitsa. Uzani moyo wanga kuti, “Ine ndine chipulumutso chako.”
Effunde frameam, et conclude adversus eos, qui persequuntur me: dic animæ meæ: Salus tua ego sum.
4 Iwo amene akufunafuna moyo wanga anyozedwe ndi kuchita manyazi; iwo amene akukonza kuti moyo wanga uwonongeke abwerere mʼmbuyo mochititsa mantha.
Confundantur et revereantur, quærentes animam meam. Avertantur retrorsum, et confundantur cogitantes mihi mala.
5 Akhale ngati mankhusu owuluka ndi mphepo pamene mngelo wa Yehova akuwapirikitsa.
Fiant tamquam pulvis ante faciem venti: et angelus Domini coarctans eos.
6 Njira yawo ikhale ya mdima ndi yoterera pamene mngelo wa Yehova akuwathamangitsa.
Fiat via illorum tenebræ et lubricum: et angelus Domini persequens eos.
7 Popeza ananditchera ukonde popanda chifukwa ndipo popanda chifukwa andikumbira dzenje,
Quoniam gratis absconderunt mihi interitum laquei sui: supervacue exprobraverunt animam meam.
8 chiwonongeko chiwapeza modzidzimutsa ukonde umene iwo abisa uwakole, agwere mʼdzenje kuti awonongedwe.
Veniat illi laqueus, quem ignorat: et captio, quam abscondit, apprehendat eum: et in laqueum cadat in ipsum.
9 Pamenepo moyo wanga udzakondwera mwa Yehova ndi kusangalala ndi chipulumutso chake.
Anima autem mea exultabit in Domino: et delectabitur super salutari suo.
10 Thupi langa lidzafuwula mokondwera, “Ndani angafanane nanu Yehova? Mumalanditsa osauka kwa amene ali ndi mphamvu zambiri, osauka ndi osowa kwa iwo amene amawalanda.”
Omnia ossa mea dicent: Domine, quis similis tibi? Eripiens inopem de manu fortiorum eius: egenum et pauperem a diripientibus eum.
11 Mboni zopanda chisoni zinayimirira, zinandifunsa zinthu zimene sindikuzidziwa.
Surgentes testes iniqui, quæ ignorabam interrogabant me.
12 Iwo anandibwezera zoyipa pa zabwino ndipo anasiya moyo wanga pa chisoni.
Retribuebant mihi mala pro bonis: sterilitatem animæ meæ.
13 Koma pamene iwo ankadwala, ine ndinavala chiguduli ndi kudzichepetsa ndekha posala zakudya. Pamene mapemphero anga anabwerera kwa ine osayankhidwa,
Ego autem cum mihi molesti essent, induebar cilicio. Humiliabam in ieiunio animam meam: et oratio mea in sinu meo convertetur.
14 ndinayendayenda ndi kulira maliro, kumulira ngati bwenzi langa kapena mʼbale wanga. Ndinaweramitsa mutu wanga mosweka mtima kukhala ngati ndikulira amayi anga.
Quasi proximum, et quasi fratrem nostrum, sic complacebam: quasi lugens et contristatus sic humiliabar.
15 Koma pamene ndinaphunthwa, iwo anasonkhana mosangalala; ondithira nkhondo anasonkhana kutsutsana nane, ineyo osadziwa. Iwo sanasiye kundiyankhulira mawu onyoza.
Et adversum me lætati sunt, et convenerunt: congregata sunt super me flagella, et ignoravi.
16 Monga anthu osapembedza, iwo anandinyoza mwachipongwe; anandikukutira mano awo.
Dissipati sunt, nec compuncti, tentaverunt me, subsannaverunt me subsannatione: frenduerunt super me dentibus suis.
17 Ambuye, mpaka liti mudzakhala mukungoyangʼana? Landitsani moyo wanga ku chiwonongeko chawo, moyo wanga wopambana ku mikango.
Domine quando respicies? restitue animam meam a malignitate eorum, a leonibus unicam meam.
18 Ndidzakuyamikani mu msonkhano waukulu; pakati pa gulu lalikulu la anthu ndidzakutamandani.
Confitebor tibi in ecclesia magna, in populo gravi laudabo te.
19 Musalole adani anga onyenga akondwere chifukwa cha masautso anga; musalole kuti amene amadana nane popanda chifukwa andiyangʼane chamʼmbali mondinyoza.
Non supergaudeant mihi qui adversantur mihi inique: qui oderunt me gratis et annuunt oculis.
20 Iwowo sayankhula mwamtendere, koma amaganizira zonamizira iwo amene amakhala mwabata mʼdziko.
Quoniam mihi quidem pacifice loquebantur: et in iracundia terræ loquentes, dolos cogitabant.
21 Iwo amandiseka mofuwula ndipo amati, “Haa! Haa! Ndipo ndi maso athuwa ife taziona.”
Et dilataverunt super me os suum: dixerunt: Euge, euge, viderunt oculi nostri.
22 Yehova mwaona zimenezi; musakhale chete. Ambuye musakhale kutali ndi ine.
Vidisti Domine, ne sileas: Domine ne discedas a me.
23 Dzukani, ndipo nyamukani kunditeteza! Mulimbane nawo chifukwa cha ine, Mulungu wanga ndi Ambuye anga.
Exurge et intende iudicio meo: Deus meus, et Dominus meus in causam meam.
24 Onetsani kusalakwa kwanga mwa chilungamo chanu, Inu Yehova Mulungu wanga. Musalole kuti akondwere chifukwa cha mavuto anga.
Iudica me secundum iustitiam tuam Domine Deus meus, et non supergaudeant mihi.
25 Musalole kuti aganize kuti, “Amati atani, zachitika monga momwe timafunira!” Kapena kunena kuti, “Tamutha ameneyu basi.”
Non dicant in cordibus suis: Euge, euge, animæ nostræ: nec dicant: Devoravimus eum.
26 Onse amene amakondwera ndi masautso anga achite manyazi ndi kusokonezeka. Onse amene amadzikweza kufuna kundipambana, avekedwe manyazi ndi mnyozo ngati zovala.
Erubescant et revereantur simul, qui gratulantur malis meis. Induantur confusione et reverentia qui magna loquuntur super me.
27 Koma amene amakondwera chifukwa chakuti ndine wosalakwa, afuwule mwachimwemwe ndi chisangalalo. Nthawi zonse azinena kuti, “Yehova akwezeke, Iye amene amakondwera ndi kupeza bwino kwa mtumiki wake.”
Exultent et lætentur qui volunt iustitiam meam: et dicant semper: Magnificetur Dominus, qui volunt pacem servi eius.
28 Pakamwa panga padzayankhula za chilungamo chanu ndi za matamando anu tsiku lonse.
Et lingua mea meditabitur iustitiam tuam, tota die laudem tuam.