< Masalimo 34 >

1 Salimo la Davide. Pamene iye ananyengezera misala pamaso pa Abimeleki, amene anamupirikitsa, iyeyo nʼkuchoka. Ndidzayamika Yehova nthawi zonse; matamando ake adzakhala pa milomo yanga nthawi zonse.
Bendeciré a Yavé en todo tiempo. Su alabanza estará de continuo en mi boca.
2 Moyo wanga udzanyadira Yehova; anthu osautsidwa amve ndi kukondwera.
En Yavé se gloriará mi alma. Lo oirán los mansos y se alegrarán.
3 Lemekezani Yehova pamodzi ndi ine; tiyeni pamodzi tikuze dzina lake.
Engrandezcan a Yavé conmigo, Y exaltemos juntos su Nombre.
4 Ine ndinafunafuna Yehova ndipo Iye anandiyankha; anandilanditsa ku mantha anga onse.
Busqué a Yavé y Él me respondió, Y me libró de todos mis temores.
5 Iwo amene amayangʼana kwa Iye, nkhope zawo zimanyezimira; nkhope zawo sizikhala zophimbidwa ndi manyazi.
Los que miraron a Él fueron iluminados, Y sus semblantes nunca serán avergonzados.
6 Munthu wosauka uno anayitana, ndipo Yehova anamumva; Yehova anamupulumutsa ku mavuto ake onse.
Este pobre clamó, Y Yavé lo escuchó, Y lo salvó de todas sus angustias.
7 Mngelo wa Yehova amatchinjiriza amene amakonda Iye ndi kuwalanditsa.
El Ángel de Yavé acampa alrededor de los que le temen, Y los rescata.
8 Lawani ndipo onani kuti Yehova ndi wabwino; wodala munthu amene amathawira kwa Iye.
Prueben y vean que Yavé es bueno. ¡Cuán feliz es el varón que confía en Él!
9 Wopani Yehova inu oyera mtima ake, pakuti iwo amene amaopa Iye sasowa kanthu.
Teman a Yavé, ustedes sus santos, Porque nada falta a los que le temen.
10 Mikango itha kulefuka ndi kumva njala koma iwo amene amafunafuna Yehova sasowa kanthu kalikonse kabwino.
Los cachorros de león necesitan y sufren hambre, Pero los que buscan a Yavé no carecen de ningún bien.
11 Bwerani ana anga, mundimvere; ndidzakuphunzitsani kuopa Yehova.
Vengan, hijos, escúchenme. Les enseñaré el temor a Yavé.
12 Aliyense wa inu amene amakonda moyo wake ndi kukhumba kuti aone masiku abwino ambiri,
¿Quién es el hombre que desea vida, Que desea muchos días para ver el bien?
13 asunge lilime lake ku zoyipa ndi milomo yake kuti isayankhule zonama.
Guarda tu boca del mal Y tus labios de hablar engaño.
14 Tembenuka kuchoka ku zoyipa ndipo chita zabwino; funafuna mtendere ndi kuwulondola.
Apártate del mal y haz el bien. Busca la paz y persíguela.
15 Maso a Yehova ali pa olungama ndipo makutu ake ali tcheru kumva kulira kwawo;
Los ojos de Yavé están hacia los justos, Y sus oídos atentos al clamor de ellos.
16 nkhope ya Yehova ikutsutsana ndi amene amachita zoyipa, kuwachotsa kuti asawakumbukirenso pa dziko lapansi.
El rostro de Yavé está contra los perversos, Para cortar su memoria de la tierra.
17 Olungama amafuwula, ndipo Yehova amawamva; Iye amawalanditsa ku mavuto awo onse.
Claman los justos, Y Yavé los oye Y los libra de todas sus angustias.
18 Yehova ali pafupi kwa osweka mtima ndipo amapulumutsa iwo amene asweka mu mzimu.
Cercano está Yavé a los quebrantados de corazón, Y salva a los contritos de espíritu.
19 Munthu wolungama atha kukhala ndi mavuto ambiri, Koma Yehova amamulanditsa ku mavuto onsewo,
Muchas son las aflicciones del justo, Pero de todas ellas lo libra Yavé.
20 Iye amateteza mafupa ake onse, palibe limodzi la mafupawo limene lidzathyoledwa.
Él guarda todos sus huesos. Ni uno de ellos es quebrado.
21 Choyipa chidzapha anthu oyipa; adani a olungama adzapezeka olakwa.
Matará al malo la maldad, Y los que aborrecen al justo serán culpables.
22 Yehova amawombola atumiki ake; aliyense amene amathawira kwa Iye sadzapezeka wolakwa.
Yavé redime la vida de sus esclavos. No serán condenados cuantos en Él confían.

< Masalimo 34 >