< Masalimo 33 >
1 Imbirani Yehova mokondwera Inu olungama, nʼkoyenera kuti owongoka mtima azitamanda Iyeyo.
2 Mutamandeni Yehova ndi pangwe; muyimbireni Iye nyimbo pa zeze wa zingwe khumi.
3 Muyimbireni nyimbo yatsopano; imbani mwaluso, ndipo fuwulani mwachimwemwe.
4 Pakuti mawu a Yehova ndi olungama ndi owona; Iye ndi wokhulupirika pa zonse zimene amachita.
5 Yehova amakonda chilungamo ndipo amaweruza molungama; dziko lapansi ladzaza ndi chikondi chake chosatha.
6 Ndi mawu a Yehova mayiko akumwamba anapangidwa, zolengedwa zake ndi mpweya wa mʼkamwa mwake.
7 Iye amasonkhanitsa pamodzi madzi a mʼnyanja mʼmitsuko; amayika zozama mʼnyumba zosungiramo.
8 Dziko lonse lapansi liope Yehova; anthu onse amulemekeze Iye.
9 Pakuti Iye anayankhula ndipo zinakhalapo; Iye analamulira ndipo zinakhazikika.
10 Yehova amalepheretsa chikonzero cha anthu a mitundu ina; Iye amaphwanya zolinga za anthu ambiri.
11 Koma chikonzero cha Yehova chimakhala mpaka muyaya, zolinga za mu mtima mwake pa mibado yonse.
12 Wodala mtundu wa anthu umene Mulungu wake ndi Yehova, anthu amene Iye anawasankha kukhala cholowa chake.
13 Kuchokera kumwamba Yehova amayangʼana pansi ndi kuona anthu onse;
14 kuchokera ku malo ake okhalako Iye amayangʼanira onse amene amakhala pa dziko lapansi.
15 Iye amene amapanga mitima ya onse, amaona zonse zimene akuchita.
16 Palibe mfumu imene imapulumutsidwa chifukwa cha kukula kwa gulu lake lankhondo; palibe msilikali amene amathawa ndi mphamvu zake zazikulu.
17 Kavalo ndi chiyembekezo cha chabechabe cha chipulumutso, ngakhale ali ndi mphamvu yayikulu sangathe kupulumutsa.
18 Koma maso a Yehova ali pa iwo amene amaopa Iye; amene chiyembekezo chawo chili mʼchikondi chake chosatha,
19 kuwawombola iwo ku imfa ndi kuwasunga ndi moyo nthawi ya njala.
20 Ife timadikira kwa Yehova mwachiyembekezo; Iye ndiye thandizo lathu ndi chishango chathu.
21 Mwa Iye mitima yathu imakondwera, pakuti ife timadalira dzina lake loyera.
22 Chikondi chanu chosatha chikhale pa ife Inu Yehova, pamene tikuyembekeza kwa Inu.