< Masalimo 31 >

1 Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Mwa Inu Yehova, ine ndimathawiramo; musalole nʼkomwe kuti ndichititsidwe manyazi; mundipulumutse chifukwa cha chilungamo chanu.
למנצח מזמור לדוד ב בך-יהוה חסיתי אל-אבושה לעולם בצדקתך פלטני
2 Tcherani khutu lanu kwa ine, bwerani msanga kudzandilanditsa; mukhale thanthwe langa lothawirapo, linga lolimba kundipulumutsa ine.
הטה אלי אזנך-- מהרה הצילני היה לי לצור-מעוז--לבית מצודות להושיעני
3 Popeza Inu ndinu thanthwe langa ndi linga langa, chifukwa cha dzina lanu tsogolereni ndi kundiwongolera.
כי-סלעי ומצודתי אתה ולמען שמך תנחני ותנהלני
4 Ndimasuleni mu msampha umene anditchera pakuti ndinu pothawirapo panga.
תוציאני--מרשת זו טמנו לי כי-אתה מעוזי
5 Mʼmanja mwanu ndipereka mzimu wanga; womboleni Yehova Mulungu wachoonadi.
בידך אפקיד רוחי פדית אותי יהוה--אל אמת
6 Koma ine ndimadana nawo amene amamamatira mafano achabechabe; ine ndimadalira Yehova.
שנאתי השמרים הבלי-שוא ואני אל-יהוה בטחתי
7 Ndidzakondwa ndi kusangalala mʼchikondi chanu popeza Inu munaona masautso anga ndipo mumadziwa kuwawa kwa moyo wanga.
אגילה ואשמחה בחסדך אשר ראית את-עניי ידעת בצרות נפשי
8 Inu simunandipereke kwa mdani koma mwayika mapazi anga pa malo otakasuka.
ולא הסגרתני ביד-אויב העמדת במרחב רגלי
9 Mundichitire chifundo Inu Yehova pakuti ndili pa mavuto; maso anga akulefuka ndi chisoni, mʼmoyo mwanga ndi mʼthupi mwanga momwe mukupweteka.
חנני יהוה כי צר-לי עששה בכעס עיני נפשי ובטני
10 Moyo wanga ukunyeka chifukwa cha kuwawidwa mtima ndi zaka zanga chifukwa cha kubuwula; mphamvu zanga zatha chifuwa cha masautso, ndipo mafupa anga akulefuka.
כי כלו ביגון חיי-- ושנותי באנחה כשל בעוני כחי ועצמי עששו
11 Chifukwa cha adani anga onse, ndine wonyozeka kwambiri ndi anansi anga; ndine chochititsa manyazi kwa abwenzi anga. Iwo amene amandiona mu msewu amandithawa.
מכל-צררי הייתי חרפה ולשכני מאד-- ופחד למידעי ראי בחוץ-- נדדו ממני
12 Ine ndinayiwalika kwa iwo ngati kuti ndinamwalira; ndakhala ngati mʼphika wosweka.
נשכחתי כמת מלב הייתי ככלי אבד
13 Pakuti ine ndamva zonena zoyipa za anthu ambiri; zoopsa zandizungulira mbali zonse; iwo akukonza chiwembu kuti alimbane nane, kuti atenge moyo wanga.
כי שמעתי דבת רבים-- מגור מסביב בהוסדם יחד עלי לקחת נפשי זממו
14 Koma ndikudalira Inu Yehova; ndikunena kuti, “Ndinu Mulungu wanga.”
ואני עליך בטחתי יהוה אמרתי אלהי אתה
15 Masiku anga ali mʼmanja mwanu; ndipulumutseni kwa adani anga ndi kwa iwo amene akundithamangitsa.
בידך עתתי הצילני מיד-אויבי ומרדפי
16 Walitsani nkhope yanu pa mtumiki wanu; pulumutseni mwa chikondi chanu chosatha.
האירה פניך על-עבדך הושיעני בחסדך
17 Yehova musalole kuti ndichite manyazi, pakuti ndalirira kwa Inu; koma oyipa achititsidwe manyazi ndipo agone chete mʼmanda. (Sheol h7585)
יהוה--אל-אבושה כי קראתיך יבשו רשעים ידמו לשאול (Sheol h7585)
18 Milomo yawo yabodzayo ikhale chete, pakuti chifukwa cha kunyada ayankhula modzikuza kutsutsana ndi wolungama.
תאלמנה שפתי-שקר הדברות על-צדיק עתק--בגאוה ובוז
19 Ndi waukulu ubwino wanu umene mwawasungira amene amakuopani, umene mumapereka anthu akuona kwa iwo amene amathawira kwa Inu.
מה רב-טובך אשר-צפנת ליראיך פעלת לחסים בך נגד בני אדם
20 Mu mthunzi wa pamalo popezeka panu muwabisa, kuwateteza ku ziwembu za anthu; mʼmalo anu okhalamo mumawateteza kwa anthu owatsutsa.
תסתירם בסתר פניך-- מרכסי-איש תצפנם בסכה מריב לשנות
21 Matamando akhale kwa Yehova, pakuti anaonetsa chikondi chake chodabwitsa kwa ine pamene ndinali mu mzinda wozingidwa.
ברוך יהוה כי הפליא חסדו לי בעיר מצור
22 Ndili mʼnkhawa zanga ndinati, “Ine ndachotsedwa pamaso panu!” Komabe Inu munamva kupempha chifundo kwanga pamene ndinapempha thandizo kwa Inu.
ואני אמרתי בחפזי-- נגרזתי מנגד עיניך אכן--שמעת קול תחנוני בשועי אליך
23 Kondani Yehova oyera mtima ake onse! Yehova amasunga wokhulupirika koma amalanga kwathunthu anthu odzikuza.
אהבו את-יהוה כל-חסידיו אמונים נצר יהוה ומשלם על-יתר עשה גאוה
24 Khalani ndi nyonga ndipo limbani mtima, inu nonse amene mumayembekezera Yehova.
חזקו ויאמץ לבבכם-- כל-המיחלים ליהוה

< Masalimo 31 >