< Masalimo 30 >

1 Salimo la Davide. Nyimbo yoyimba popereka Nyumba ya Mulungu. Ndidzakukwezani Yehova, chifukwa mwanditulutsa kwakuya, ndipo simunalole kuti adani anga akondwere pa ine.
מזמור שיר-חנכת הבית לדוד ב ארוממך יהוה כי דליתני ולא-שמחת איבי לי
2 Inu Yehova Mulungu wanga ndinapempha kwa Inu thandizo ndipo Inu munandichiritsa.
יהוה אלהי-- שועתי אליך ותרפאני
3 Inu Yehova, munanditulutsa ku manda, munandisunga kuti ndisatsalire mʼdzenje. (Sheol h7585)
יהוה--העלית מן-שאול נפשי חייתני מיורדי- (מירדי-) בור (Sheol h7585)
4 Imbirani Yehova inu anthu ake okhulupirika; tamandani dzina lake loyera.
זמרו ליהוה חסידיו והודו לזכר קדשו
5 Pakuti mkwiyo wake umakhala kwa kanthawi koma kukoma mtima kwake ndi kwa moyo wonse; utha kuchezera kulira usiku wonse, koma chimwemwe chimabwera mmawa.
כי רגע באפו-- חיים ברצונו בערב ילין בכי ולבקר רנה
6 Pamene ndinaona kuti ndili otetezedwa ndinati, “Sindidzagwedezekanso.”
ואני אמרתי בשלוי-- בל-אמוט לעולם
7 Inu Yehova, pamene munandikomera mtima, munachititsa phiri langa kuyima chilili; koma pamene munabisa nkhope yanu, ndinataya mtima.
יהוה-- ברצונך העמדתה להררי-עז הסתרת פניך הייתי נבהל
8 Kwa Inu Yehova ndinayitana; kwa Ambuye ndinapempha chifundo;
אליך יהוה אקרא ואל-אדני אתחנן
9 “Kodi pali phindu lanji powonongeka kwanga ngati nditsikira ku dzenje? Kodi fumbi lidzakutamandani Inu? Kodi lidzalengeza za kukhulupirika kwanu?
מה-בצע בדמי ברדתי אל-שחת היודך עפר היגיד אמתך
10 Imvani Yehova ndipo mundichitire chifundo; Yehova mukhale thandizo langa.”
שמע-יהוה וחנני יהוה היה-עזר לי
11 Inu munasandutsa kulira kwanga kukhala kuvina; munachotsa chiguduli changa ndi kundiveka ndi chimwemwe,
הפכת מספדי למחול לי פתחת שקי ותאזרני שמחה
12 kuti mtima wanga uthe kuyimbira Inu usakhale chete. Yehova Mulungu wanga, ndidzapereka kwa Inu mayamiko kwamuyaya.
למען יזמרך כבוד-- ולא ידם יהוה אלהי לעולם אודך

< Masalimo 30 >