< Masalimo 3 >
1 Salimo la Davide. Atathawa mwana wake Abisalomu. Inu Yehova, achulukadi adani anga! Achulukadi amene andiwukira!
大衛逃避他兒子押沙龍的時候作的詩。 耶和華啊,我的敵人何其加增; 有許多人起來攻擊我。
2 Ambiri akunena za ine kuti, “Mulungu sadzamupulumutsa.” (Sela)
有許多人議論我說: 他得不着上帝的幫助。 (細拉)
3 Koma Inu Yehova, ndinu chishango chonditeteza, Inu mwandiveka ulemerero ndipo mwanditukula.
但你-耶和華是我四圍的盾牌, 是我的榮耀,又是叫我抬起頭來的。
4 Kwa Yehova, Ine ndilira mofuwula ndipo Iye amandiyankha kuchokera ku phiri lake loyera. (Sela)
我用我的聲音求告耶和華, 他就從他的聖山上應允我。 (細拉)
5 Ine ndimagona ndi kupeza tulo; ndimadzukanso chifukwa Yehova amandichirikiza.
我躺下睡覺,我醒着, 耶和華都保佑我。
6 Sindidzaopa adani anga osawerengeka amene abwera kulimbana nane kuchokera ku madera onse.
雖有成萬的百姓來周圍攻擊我, 我也不怕。
7 Dzukani, Inu Yehova! Pulumutseni, Inu Mulungu wanga. Akantheni adani anga onse pa msagwada; gululani mano a anthu oyipa.
耶和華啊,求你起來! 我的上帝啊,求你救我! 因為你打了我一切仇敵的腮骨, 敲碎了惡人的牙齒。
8 Chipulumutso chimachokera kwa Yehova. Madalitso akhale pa anthu anu. (Sela)
救恩屬乎耶和華; 願你賜福給你的百姓。 (細拉)