< Masalimo 29 >
1 Salimo la Davide. Perekani kwa Yehova, inu anthu amphamvu, perekani kwa Yehova ulemerero ndi mphamvu.
A Psalm by David. Ascribe to Yahweh, you sons of the mighty, ascribe to Yahweh glory and strength.
2 Perekani kwa Yehova ulemerero woyenera dzina lake, pembedzani Yehova mwa kukongola kwa chiyero chake.
Ascribe to Yahweh the glory due to his name. Worship Yahweh in holy array.
3 Liwu la Yehova lili pamwamba pa madzi; Mulungu waulemerero abangula, Yehova abangula pamwamba pa madzi amphamvu.
Yahweh’s voice is on the waters. The God of glory thunders, even Yahweh on many waters.
4 Liwu la Yehova ndi lamphamvu; liwu la Yehova ndi laulemerero.
Yahweh’s voice is powerful. Yahweh’s voice is full of majesty.
5 Liwu la Yehova limathyola mikungudza; Yehova amathyolathyola mikungudza ya ku Lebanoni.
Yahweh’s voice breaks the cedars. Yes, Yahweh breaks in pieces the cedars of Lebanon.
6 Iye amachititsa Lebanoni kulumphalumpha ngati mwana wangʼombe, Siriyoni ngati mwana wa njati:
He makes them also to skip like a calf; Lebanon and Sirion like a young, wild ox.
7 Liwu la Yehova limakantha ngati kungʼanima kwa mphenzi.
Yahweh’s voice strikes with flashes of lightning.
8 Liwu la Yehova limagwedeza chipululu; Yehova amagwedeza chipululu cha Kadesi.
Yahweh’s voice shakes the wilderness. Yahweh shakes the wilderness of Kadesh.
9 Liwu la Yehova limapindapinda mibawa ndi kuyeretsa nkhalango. Ndipo mʼNyumba mwake onse amafuwula kuti, “Ulemerero!”
Yahweh’s voice makes the deer calve, and strips the forests bare. In his temple everything says, “Glory!”
10 Yehova amakhala pamwamba pa madzi osefukira, Yehova ndiye mfumu kwamuyaya.
Yahweh sat enthroned at the Flood. Yes, Yahweh sits as King forever.
11 Yehova amapereka mphamvu kwa anthu ake; Yehova amadalitsa anthu ake ndi mtendere.
Yahweh will give strength to his people. Yahweh will bless his people with peace.