< Masalimo 28 >

1 Salimo la Davide. Kwa Inu ine ndiyitana, Yehova ndinu Thanthwe langa; musakhale osamva kwa ine. Pakuti mukapitirira kukhala chete, ndidzakhala ngati iwo amene atsikira ku dzenje.
Von David. Zu dir, HERR, rufe ich:
2 Imvani kupempha chifundo kwanga pomwe ndikuyitana kwa Inu kuti mundithandize, pomwe ndikukweza manja anga kuloza ku malo anu oyeretsetsa.
Höre mein lautes Flehen, wenn ich zu dir schreie, wenn ich meine Hände erhebe nach deinem Allerheiligsten!
3 Musandikokere kutali pamodzi ndi anthu oyipa, pamodzi ndi iwo amene amachita zoyipa, amene amayankhula mwachikondi ndi anzawo koma akusunga chiwembu mʼmitima mwawo.
Raffe mich nicht weg mit den Frevlern und den Übeltätern, die freundlich reden mit ihren Nächsten und dabei Arges im Herzen sinnen!
4 Muwabwezere chifukwa cha zochita zawo ndi ntchito zawo zoyipa; abwezereni chifuwa cha zimene manja awo achita ndipo mubweretse pa iwo zimene zowayenera.
Vergilt du ihnen nach ihrem Tun, nach der Bosheit ihrer Handlungen, vergilt ihnen nach dem Werk ihrer Hände, zahl’ ihnen ihr Verhalten heim, wie sie’s verdienen!
5 Popeza iwowo sakhudzidwa ndi ntchito za Yehova, ndi zimene manja ake anazichita, Iye adzawakhadzula ndipo sadzawathandizanso.
Denn sie achten nicht auf das Walten des HERRN und das Werk seiner Hände; drum wird er sie niederreißen und nicht wieder aufbaun.
6 Matamando apite kwa Yehova, popeza Iye wamva kupempha chifundo kwanga.
Gepriesen sei der HERR, denn er hat gehört meinen lauten Hilferuf!
7 Yehova ndiye mphamvu yanga ndi chishango changa; mtima wanga umadalira Iye, ndipo Ine ndathandizidwa. Mtima wanga umalumphalumpha chifukwa cha chimwemwe ndipo ndidzayamika Iye mʼnyimbo.
Der HERR ist meine Stärke und mein Schild; auf ihn hat mein Herz vertraut, da ist mir Hilfe geworden. So frohlockt denn mein Herz, und mit meinem Liede will ich ihm danken.
8 Yehova ndi mphamvu ya anthu ake, linga la chipulumutso kwa wodzozedwa wake.
Der HERR ist seines Volkes Stärke und seines Gesalbten rettende Zuflucht.
9 Pulumutsani anthu anu ndipo mudalitse cholowa chanu; mukhale mʼbusa wawo ndipo muwakweze kwamuyaya.
O hilf deinem Volk und segne dein Erbe, weide sie und trage sie ewiglich!

< Masalimo 28 >