< Masalimo 27 >
1 Salimo la Davide. Yehova ndiye kuwunika kwanga ndi chipulumutso changa; ndidzaopa yani? Yehova ndi linga la moyo wanga; ndidzachita mantha ndi yani?
De David. Yahvé es mi luz y mi socorro; ¿a quién temeré? La defensa de mi vida es Yahvé; ¿ante quién podré temblar?
2 Pamene anthu oyipa abwera kudzalimbana nane kudzadya mnofu wanga, pamene adani anga ndi achiwembu andithira nkhondo, iwo adzapunthwa ndi kugwa.
Cada vez que me asaltan los malignos para devorar mi carne, son ellos, mis adversarios y enemigos, quienes vacilan y caen.
3 Ngakhale gulu lankhondo lindizinge, mtima wanga sudzaopa. Ngakhale nkhondo itayambika kulimbana nane, ngakhale nthawi imeneyo, ine ndidzalimbika mtima.
Si un ejército acampase contra mí, mi corazón no temería; y aunque estalle contra mí la guerra, tendré confianza.
4 Chinthu chimodzi chokha chimene ndipempha kwa Yehova, ichi ndi chimene ndidzachifunafuna: kuti ndikhale mʼNyumba ya Yehova masiku onse a moyo wanga, ndi kuyangʼana kukongola kwa Yehova, ndi kumufunafuna Iye mʼNyumba yake.
Una sola cosa he pedido a Yahvé, y esto sí lo reclamo: [habitar en la casa de Yahvé todos los días de mi vida]; contemplar la suavidad de Yahvé y meditar en su santuario.
5 Pakuti pa tsiku la msautso Iye adzanditeteza mʼmalo ake okhalamo; adzandibisa mʼkati mwa Nyumba yake ndi kukhazika ine pamwamba pa thanthwe.
Porque en el día malo Él me esconderá en su tienda; me tendrá seguro en el secreto de su tabernáculo, y me pondrá sobre una alta roca.
6 Kotero mutu wanga udzakwezedwa kuposa adani anga amene andizungulira; pa Nyumba yake ndidzapereka nsembe ndi mfuwu wachimwemwe; ndidzayimba nyimbo kwa Yehova.
Entonces mi cabeza se alzará por encima de mis enemigos en torno mío, e inmolaré en su tabernáculo sacrificios de júbilo; cantaré y entonaré salmos a Yahvé.
7 Imvani mawu anga pamene ndiyitana Inu Yehova mundichitire chifundo ndipo mundiyankhe.
Escucha, oh Yahvé, mi voz que te llama; ten misericordia de mí y atiéndeme.
8 Mtima wanga ukuti kwa Inu, “Funafuna nkhope yake!” Nkhope yanu Yehova ndidzayifunafuna.
Mi corazón sabe que Tú has dicho: “Buscadme.” Y yo busco tu rostro, oh Yahvé.
9 Musandibisire nkhope yanu, musamubweze mtumiki wanu mwamkwiyo; mwakhala muli thandizo langa. Musandikane kapena kunditaya, Inu Mulungu Mpulumutsi wanga.
No quieras esconderme tu faz, no rechaces con desdén a tu siervo. Mi socorro eres Tú; no me eches fuera, ni me desampares, oh Dios, Salvador mío.
10 Ngakhale abambo ndi amayi anga anditaya Yehova adzandisamala.
Si mi padre y mi madre me abandonan, Yahvé me recogerá.
11 Phunzitseni njira yanu Inu Yehova, munditsogolere mʼnjira yowongoka chifukwa cha ondizunza.
Muéstrame, oh Yahvé, tu camino, y condúceme por la senda llana a causa de los que me están asechando.
12 Musandipereke ku zokhumba za adani anga, pakuti mboni zambiri zauka kutsutsana nane ndipo zikundiopseza.
No me dejes entregado a la voluntad de mis enemigos, porque se han levantado contra mí falsos testigos que respiran crueldad.
13 Ine ndikutsimikiza mtima za zimenezi; ndidzaona ubwino wa Yehova mʼdziko la anthu amoyo.
¡Ah, si no creyera yo que veré los bienes de Yahvé en la tierra de los vivientes!
14 Dikirani pa Yehova; khalani anyonga ndipo limbani mtima nimudikire Yehova.
¡Aguarda a Yahvé y ten ánimo; aliéntese tu corazón y aguarde a Yahvé!