< Masalimo 26 >
1 Salimo la Davide. Weruzeni Inu Yehova pakuti ndakhala moyo wosalakwa. Ndadalira Yehova popanda kugwedezeka.
Judge me, O Jehovah, for I have walked in my integrity. I have also trusted in Jehovah without wavering.
2 Patseni mayeso, Inu Yehova ndipo ndiyeseni, santhulani mtima wanga ndi maganizo anga;
Examine me, O Jehovah, and prove me. Try my heart and my mind.
3 pakuti chikondi chanu chili pamaso panga nthawi zonse, ndipo ndimayenda mʼchoonadi chanu nthawi zonse.
For thy loving kindness is before my eyes, and I have walked in thy truth.
4 Ine sindikhala pansi pamodzi ndi anthu achinyengo, kapena kufunsa nzeru kwa achiphamaso.
I have not sat with men of falsehood, nor will I go in with dissemblers.
5 Ndimanyansidwa ndi msonkhano wa anthu ochita zoyipa ndipo ndimakana kukhala pansi pamodzi ndi oyipa.
I hate the assembly of evildoers, and will not sit with the wicked.
6 Ndimasamba mʼmanja mwanga kuonetsa kusalakwa kwanga ndi kupita kukatumikira pa guwa lanu la nsembe, Inu Yehova,
I will wash my hands in innocence, so I will encompass thine altar, O Jehovah,
7 kulengeza mofuwula za matamando anu ndi kuwuza onse za ntchito zanu zodabwitsa.
that I may make the voice of thanksgiving to be heard, and tell of all thy wondrous works.
8 Ndimakonda Nyumba imene Inu Yehova mumakhalamo, malo amene ulemerero wanu umapezekako.
Jehovah, I love the habitation of thy house, and the place where thy glory dwells.
9 Musachotse moyo wanga pamodzi ndi ochimwa, moyo wanga pamodzi ndi anthu akupha anzawo,
Gather not my soul with sinners, nor my life with men of blood,
10 amene mʼmanja mwawo muli ndondomeko zoyipa, dzanja lawo lamanja ladzaza ndi ziphuphu.
in whose hands is wickedness, and their right hand is full of bribes.
11 Koma ine ndimakhala moyo wosalakwa; mu msonkhano wa anthu anu ndidzatamanda Yehova.
But as for me, I will walk in my integrity. Redeem me, and be merciful to me.
12 Ndayima pa malo wopanda zovuta ndipo ndidzatamanda Yehova mu msonkhano waukulu.
My foot stands in an even place. In the congregations I will bless Jehovah.