< Masalimo 25 >

1 Salimo la Davide. Kwa Inu Yehova, ndipereka moyo wanga.
לְדָוִ֡ד אֵלֶ֥יךָ יְ֝הוָ֗ה נַפְשִׁ֥י אֶשָּֽׂא׃
2 Ndimadalira Inu Mulungu wanga. Musalole kuti ndichite manyazi kapena kuti adani anga andipambane.
אֱֽלֹהַ֗י בְּךָ֣ בָ֭טַחְתִּי אַל־אֵב֑וֹשָׁה אַל־יַֽעַלְצ֖וּ אֹיְבַ֣י לִֽי׃
3 Aliyense amene amayembekezera kwa Ambuye sadzachititsidwa manyazi koma achinyengo ndiwo adzachititsidwe manyazi ndipo sadzakhala ndi chodzitetezera.
גַּ֣ם כָּל־קֹ֭וֶיךָ לֹ֣א יֵבֹ֑שׁוּ יֵ֝בֹ֗שׁוּ הַבּוֹגְדִ֥ים רֵיקָֽם׃
4 Ndidziwitseni njira zanu Inu Yehova, phunzitseni mayendedwe anu;
דְּרָכֶ֣יךָ יְ֭הוָה הוֹדִיעֵ֑נִי אֹ֖רְחוֹתֶ֣יךָ לַמְּדֵֽנִי׃
5 tsogolereni mʼchoonadi chanu ndi kundiphunzitsa, pakuti Inu ndinu Mulungu mpulumutsi wanga, ndipo chiyembekezo changa chili mwa Inu tsiku lonse.
הַדְרִ֘יכֵ֤נִי בַאֲמִתֶּ֨ךָ ׀ וְֽלַמְּדֵ֗נִי כִּֽי־אַ֭תָּה אֱלֹהֵ֣י יִשְׁעִ֑י אוֹתְךָ֥ קִ֝וִּ֗יתִי כָּל־הַיּֽוֹם׃
6 Kumbukirani Inu Yehova chifundo ndi chikondi chanu chachikulu, pakuti ndi zakalekale.
זְכֹר־רַחֲמֶ֣יךָ יְ֭הוָה וַחֲסָדֶ֑יךָ כִּ֖י מֵעוֹלָ֣ם הֵֽמָּה׃
7 Musakumbukire machimo a ubwana wanga ndi makhalidwe anga owukira; molingana ndi chikondi chanu ndikumbukireni ine, pakuti Inu Yehova ndinu wabwino.
חַטֹּ֤אות נְעוּרַ֨י ׀ וּפְשָׁעַ֗י אַל־תִּ֫זְכֹּ֥ר כְּחַסְדְּךָ֥ זְכָר־לִי־אַ֑תָּה לְמַ֖עַן טוּבְךָ֣ יְהוָֽה׃
8 Yehova ndi wabwino ndi wolungama; choncho Iye akulangiza ochimwa mʼnjira yake.
טוֹב־וְיָשָׁ֥ר יְהוָ֑ה עַל־כֵּ֤ן יוֹרֶ֖ה חַטָּאִ֣ים בַּדָּֽרֶךְ׃
9 Amatsogolera odzichepetsa kuti achite zolungama ndipo amawaphunzitsa njira zake.
יַדְרֵ֣ךְ עֲ֭נָוִים בַּמִּשְׁפָּ֑ט וִֽילַמֵּ֖ד עֲנָוִ֣ים דַּרְכּֽוֹ׃
10 Njira zonse za Yehova ndi zachikondi ndi zokhulupirika kwa iwo amene amasunga zofuna za pangano lake.
כָּל־אָרְח֣וֹת יְ֭הוָה חֶ֣סֶד וֶאֱמֶ֑ת לְנֹצְרֵ֥י בְ֝רִית֗וֹ וְעֵדֹתָֽיו׃
11 Chifukwa cha dzina lanu, Inu Yehova, khululukireni mphulupulu zanga, ngakhale kuti ndi zochuluka.
לְמַֽעַן־שִׁמְךָ֥ יְהוָ֑ה וְֽסָלַחְתָּ֥ לַ֝עֲוֺנִ֗י כִּ֣י רַב־הֽוּא׃
12 Tsono ndani munthu amene amaopa Yehova? Yehova adzamulangiza njira yoti ayitsate.
מִי־זֶ֣ה הָ֭אִישׁ יְרֵ֣א יְהוָ֑ה י֝וֹרֶ֗נּוּ בְּדֶ֣רֶךְ יִבְחָֽר׃
13 Iye adzakhala pa ulemerero masiku ake onse, ndipo zidzukulu zake zidzalandira dziko ngati cholowa chawo.
נַ֭פְשׁוֹ בְּט֣וֹב תָּלִ֑ין וְ֝זַרְע֗וֹ יִ֣ירַשׁ אָֽרֶץ׃
14 Yehova amawulula chinsinsi chake kwa iwo amene amamuopa; amawulula pangano lake kwa iwowo.
ס֣וֹד יְ֭הוָה לִירֵאָ֑יו וּ֝בְרִית֗וֹ לְהוֹדִיעָֽם׃
15 Maso anga ali pa Yehova nthawi zonse, pakuti ndi Iye yekha amene adzawonjola mapazi anga mu msampha.
עֵינַ֣י תָּ֭מִיד אֶל־יְהוָ֑ה כִּ֤י הֽוּא־יוֹצִ֖יא מֵרֶ֣שֶׁת רַגְלָֽי׃
16 Tembenukirani kwa ine ndipo mundikomere mtima, pakuti ndili ndekhandekha ndipo ndikuzunzika.
פְּנֵה־אֵלַ֥י וְחָנֵּ֑נִי כִּֽי־יָחִ֖יד וְעָנִ֣י אָֽנִי׃
17 Masautso a mu mtima mwanga achulukirachulukira; masuleni ku zowawa zanga.
צָר֣וֹת לְבָבִ֣י הִרְחִ֑יבוּ מִ֝מְּצֽוּקוֹתַ֗י הוֹצִיאֵֽנִי׃
18 Penyani mazunzo anga ndi zovuta zanga ndipo mufafanize machimo anga onse.
רְאֵ֣ה עָ֭נְיִי וַעֲמָלִ֑י וְ֝שָׂ֗א לְכָל־חַטֹּאותָֽי׃
19 Onani mmene adani anga achulukira ndi momwe chidani chawo ndi ine chakulira.
רְאֵֽה־אוֹיְבַ֥י כִּי־רָ֑בּוּ וְשִׂנְאַ֖ת חָמָ֣ס שְׂנֵאֽוּנִי׃
20 Tetezani moyo wanga ndi kundilanditsa; musalole kuti ndichite manyazi, pakuti ndimathawira kwa Inu.
שָׁמְרָ֣ה נַ֭פְשִׁי וְהַצִּילֵ֑נִי אַל־אֵ֝ב֗וֹשׁ כִּֽי־חָסִ֥יתִי בָֽךְ׃
21 Kukhulupirika ndi kulungama kwanga kunditeteze, chifukwa chiyembekezo changa chili mwa Inu.
תֹּם־וָיֹ֥שֶׁר יִצְּר֑וּנִי כִּ֝֗י קִוִּיתִֽיךָ׃
22 Wombolani Israeli Inu Mulungu, ku mavuto ake onse!
פְּדֵ֣ה אֱ֭לֹהִים אֶת־יִשְׂרָאֵ֑ל מִ֝כֹּ֗ל צָֽרוֹתָיו׃

< Masalimo 25 >