< Masalimo 24 >

1 Salimo la Davide. Dziko lapansi ndi la Yehova ndi zonse zimene zili mʼmenemo, dziko ndi onse amene amakhala mʼmenemo;
A Psalm of David. The earth [is] the LORD’s, and the fulness thereof; the world, and they that dwell therein.
2 pakuti Iye ndiye anayika maziko ake pa nyanja ndi kulikhazika pamwamba pa madzi.
For he hath founded it upon the seas, and established it upon the floods.
3 Ndani angakwere phiri la Yehova? Ndani angathe kuyima pa malo ake opatulika?
Who shall ascend into the hill of the LORD? or who shall stand in his holy place?
4 Iye amene ali ndi mʼmanja moyera ndi mtima woyera, amene sapereka moyo wake kwa fano kapena kulumbira mwachinyengo.
He that hath clean hands, and a pure heart; who hath not lifted up his soul unto vanity, nor sworn deceitfully.
5 Iyeyo adzalandira madalitso kwa Yehova ndipo Mulungu mpulumutsi wake adzagamula kuti alibe mlandu.
He shall receive the blessing from the LORD, and righteousness from the God of his salvation.
6 Umenewo ndiwo mʼbado wa amene amafunafuna Yehova; amene amafunafuna nkhope yanu, Inu Mulungu wa Yakobo. (Sela)
This [is] the generation of them that seek him, that seek thy face, O Jacob. (Selah)
7 Tukulani mitu yanu inu zipata; tsekukani, inu zitseko zakalekalenu, kuti Mfumu yaulemerero ilowe.
Lift up your heads, O ye gates; and be ye lift up, ye everlasting doors; and the King of glory shall come in.
8 Kodi Mfumu yaulemereroyo ndani? Yehova Wamphamvuzonse, Yehova ndiye wamphamvu pa nkhondo.
Who [is] this King of glory? The LORD strong and mighty, the LORD mighty in battle.
9 Tukulani mitu yanu, inu zipata; tsekukani, inu zitseko zakalekalenu, kuti Mfumu yaulemerero ilowe.
Lift up your heads, O ye gates; even lift [them] up, ye everlasting doors; and the King of glory shall come in.
10 Kodi Mfumu yaulemereroyo ndani? Yehova Wamphamvuzonse, Iye ndiye Mfumu yaulemerero. (Sela)
Who is this King of glory? The LORD of hosts, he [is] the King of glory. (Selah)

< Masalimo 24 >