< Masalimo 23 >

1 Salimo la Davide. Yehova ndiye mʼbusa wanga, sindidzasowa kanthu.
מזמור לדוד יהוה רעי לא אחסר
2 Amandigoneka pa msipu wobiriwira, amanditsogolera ku madzi akumwa abwino,
בנאות דשא ירביצני על-מי מנחות ינהלני
3 amatsitsimutsa moyo wanga. Amanditsogolera mʼnjira zachilungamo chifukwa cha dzina lake.
נפשי ישובב ינחני במעגלי-צדק למען שמו
4 Ngakhale ndiyende mʼchigwa cha mdima wakuda bii, sindidzaopa choyipa, pakuti Inu muli ndi ine; chibonga chanu ndi ndodo yanu zimanditonthoza.
גם כי-אלך בגיא צלמות לא-אירא רע-- כי-אתה עמדי שבטך ומשענתך המה ינחמני
5 Mumandikonzera chakudya adani anga akuona. Mumadzoza mutu wanga ndi mafuta; chikho changa chimasefukira.
תערך לפני שלחן-- נגד צררי דשנת בשמן ראשי כוסי רויה
6 Zoonadi, zokoma ndi chikondi chosasinthika zidzanditsata masiku onse a moyo wanga, ndipo ndidzakhala mʼNyumba ya Yehova kwamuyaya.
אך טוב וחסד ירדפוני-- כל-ימי חיי ושבתי בבית-יהוה לארך ימים

< Masalimo 23 >