< Masalimo 22 >

1 Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Monga mwa “Mbawala yayikazi ya Mmawa.” Salimo la Davide. Mulungu wanga, Mulungu wanga, nʼchifukwa chiyani mwandisiya? Chifuwa chiyani simukundithandiza ndi pangʼono pomwe? Nʼchifukwa chiyani simukumva mawu a kudandaula kwanga?
למנצח על אילת השחר מזמור לדוד אלי אלי למה עזבתני רחוק מישועתי דברי שאגתי׃
2 Inu Mulungu wanga, ine ndimalira masana, koma simuyankha, usikunso, ndipo sindikhala chete.
אלהי אקרא יומם ולא תענה ולילה ולא דומיה לי׃
3 Inu ndinu Woyera, wokhala pa mpando waufumu; ndinu matamando a Israeli.
ואתה קדוש יושב תהלות ישראל׃
4 Pa inu makolo athu anadalira; iwo anadalira ndipo Inu munawapulumutsa.
בך בטחו אבתינו בטחו ותפלטמו׃
5 Analirira kwa inu ndipo munawapulumutsa. Iwo anakhulupirira Inu ndipo simunawakhumudwitse.
אליך זעקו ונמלטו בך בטחו ולא בושו׃
6 Koma ine ndine nyongolotsi osati munthu, wosekedwa ndi wonyozedwa ndi anthu onse.
ואנכי תולעת ולא איש חרפת אדם ובזוי עם׃
7 Onse amene amandiona amandiseka; amandiyankhulira mawu achipongwe akupukusa mitu yawo kunena kuti
כל ראי ילעגו לי יפטירו בשפה יניעו ראש׃
8 “Iyeyu amadalira Yehova, musiyeni Yehovayo amulanditse. Musiyeni Yehova amupulumutse popeza amakondwera mwa Yehovayo.”
גל אל יהוה יפלטהו יצילהו כי חפץ בו׃
9 Komabe Inu ndinu amene munandibadwitsa, munanditulutsa mʼmimba mwa amayi anga. Munachititsa kuti ndizikudalirani ngakhale pa nthawi imene ndinkayamwa.
כי אתה גחי מבטן מבטיחי על שדי אמי׃
10 Chibadwire ine ndinaperekedwa kwa Inu; kuchokera mʼmimba mwa amayi anga Inu mwakhala muli Mulungu wanga.
עליך השלכתי מרחם מבטן אמי אלי אתה׃
11 Musakhale kutali ndi ine, pakuti mavuto ali pafupi ndipo palibe wina wondipulumutsa.
אל תרחק ממני כי צרה קרובה כי אין עוזר׃
12 Ngʼombe zazimuna zandizungulira; ngʼombe zazimuna zamphamvu za ku Basani zandizinga.
סבבוני פרים רבים אבירי בשן כתרוני׃
13 Mikango yobangula pokadzula nyama, yatsekula kwambiri pakamwa pawo kulimbana nane.
פצו עלי פיהם אריה טרף ושאג׃
14 Ine ndatayika pansi ngati madzi ndipo mafupa anga onse achoka mʼmalo mwake. Mtima wanga wasanduka phula; wasungunuka mʼkati mwanga.
כמים נשפכתי והתפרדו כל עצמותי היה לבי כדונג נמס בתוך מעי׃
15 Mphamvu zanga zauma ngati phale, ndipo lilime langa lamamatira ku nsagwada; mwandigoneka mʼfumbi la imfa.
יבש כחרש כחי ולשוני מדבק מלקוחי ולעפר מות תשפתני׃
16 Agalu andizungulira; gulu la anthu oyipa landizinga. Alasa manja ndi mapazi anga.
כי סבבוני כלבים עדת מרעים הקיפוני כארי ידי ורגלי׃
17 Ine nditha kuwerenga mafupa anga onse; anthu amandiyangʼanitsitsa ndi kundidzuma.
אספר כל עצמותי המה יביטו יראו בי׃
18 Iwo agawana zovala zanga pakati pawo ndi kuchita maere pa zovala zangazo.
יחלקו בגדי להם ועל לבושי יפילו גורל׃
19 Koma Inu Yehova, musakhale kutali; Inu mphamvu yanga, bwerani msanga kuti mudzandithandize.
ואתה יהוה אל תרחק אילותי לעזרתי חושה׃
20 Pulumutsani moyo wanga ku lupanga, moyo wanga wopambanawu ku mphamvu ya agalu.
הצילה מחרב נפשי מיד כלב יחידתי׃
21 Ndilanditseni mʼkamwa mwa mikango; pulumutseni ku nyanga za njati.
הושיעני מפי אריה ומקרני רמים עניתני׃
22 Ine ndidzalengeza dzina lanu kwa abale anga; ndidzakutamandani mu msonkhano.
אספרה שמך לאחי בתוך קהל אהללך׃
23 Inu amene mumaopa Yehova mutamandeni! Inu zidzukulu zonse za Yakobo, mulemekezeni! Muopeni mwaulemu, inu zidzukulu zonse za Israeli!
יראי יהוה הללוהו כל זרע יעקב כבדוהו וגורו ממנו כל זרע ישראל׃
24 Pakuti Iye sanapeputse kapena kunyoza kuvutika kwa wosautsidwayo; Iye sanabise nkhope yake kwa iye. Koma anamvera kulira kwake kofuna thandizo.
כי לא בזה ולא שקץ ענות עני ולא הסתיר פניו ממנו ובשועו אליו שמע׃
25 Ndidzakutamandani pa msonkhano waukulu chifukwa cha zimene mwandichitira. Ndidzakwaniritsa lonjezo langa pamaso pa amene amaopa Inu.
מאתך תהלתי בקהל רב נדרי אשלם נגד יראיו׃
26 Osauka adzadya ndipo adzakhuta; iwo amene amafunafuna Yehova adzamutamanda. Mitima yanu ikhale ndi moyo mpaka muyaya!
יאכלו ענוים וישבעו יהללו יהוה דרשיו יחי לבבכם לעד׃
27 Malekezero onse a dziko lapansi adzakumbukira Yehova ndi kutembenukira kwa Iye, ndipo mabanja a mitundu ya anthu adzawerama pamaso pake,
יזכרו וישבו אל יהוה כל אפסי ארץ וישתחוו לפניך כל משפחות גוים׃
28 pakuti ulamuliro ndi wake wa Yehova ndipo Iye amalamulira anthu a mitundu yonse.
כי ליהוה המלוכה ומשל בגוים׃
29 Anthu olemera onse a dziko lapansi adzachita phwando ndi kulambira; onse amene amapita ku fumbi adzagwada pamaso pake; iwo amene sangathe kudzisunga okha ndi moyo.
אכלו וישתחוו כל דשני ארץ לפניו יכרעו כל יורדי עפר ונפשו לא חיה׃
30 Zidzukulu zamʼtsogolo zidzamutumikira Iye; mibado ya mʼtsogolo idzawuzidwa za Ambuye.
זרע יעבדנו יספר לאדני לדור׃
31 Iwo adzalengeza za chilungamo chake kwa anthu amene pano sanabadwe pakuti Iye wachita zimenezi.
יבאו ויגידו צדקתו לעם נולד כי עשה׃

< Masalimo 22 >