< Masalimo 20 >
1 Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Yehova akuyankhe pamene uli pa msautso; dzina la Mulungu wa Yakobo likuteteze.
For the Chief Musician. A Psalm by David. May the LORD answer you in the day of trouble. May the name of the God of Jacob set you up on high,
2 Iye atumize thandizo kuchokera ku malo ake opatulika; akugwirizize kuchokera ku Ziyoni.
send you help from the sanctuary, grant you support from Zion,
3 Iye akumbukire nsembe zako zonse ndipo alandire nsembe zako zopsereza. (Sela)
remember all your offerings, and accept your burned sacrifice. (Selah)
4 Akupatse chokhumba cha mtima wako ndipo akuthandize kuti zonse wakonza zichitike.
May he grant you your heart’s desire, and fulfill all your counsel.
5 Ife tidzafuwula ndi chimwemwe pamene iwe wapambana ndipo tidzanyamula mbendera zathu mʼdzina la Mulungu wathu, Yehova ayankhe zopempha zako zonse.
We will triumph in your salvation. In the name of our God, we will set up our banners. May the LORD grant all your requests.
6 Tsopano ndadziwa kuti Yehova amapulumutsa wodzozedwa wake; Iye amamuyankha kuchokera kumwamba ku malo ake opatulika ndi mphamvu yopulumutsa ya dzanja lake lamanja.
Now I know that the LORD saves his anointed. He will answer him from his holy heaven, with the saving strength of his right hand.
7 Ena amadalira magaleta ndipo ena akavalo koma ife tidzadalira dzina la Yehova Mulungu wathu.
Some trust in chariots, and some in horses, but we trust in the name of the LORD our God.
8 Iwo amagonjetsedwa ndi kugwa, koma ife timadzuka ndi kuyima chilili.
They are bowed down and fallen, but we rise up, and stand upright.
9 Inu Yehova, pulumutsani mfumu! Tiyankheni pamene tikuyitanani!
Save, LORD! Let the King answer us when we call!