< Masalimo 19 >
1 Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Zakumwamba zimalengeza za ulemerero wa Mulungu; thambo limalalikira ntchito za manja ake.
2 Tsiku ndi tsiku zimayankhula mawu ambiri, usiku ndi usiku zimaonetsa poyera nzeru.
3 Palibe kuyankhula, palibe mawu aliwonse; liwu lawo silimveka.
4 Koma uthenga wawo umapita pa dziko lonse lapansi, mawuwo amafika mpaka kumalekezero a dziko lapansi.
5 Dzuwa lili ngati mkwatibwi wobwera kuchokera ku nsanja yake, ngati katswiri wokondwerera kuthamanga pa mpikisano.
6 Limatuluka kuyambira mbali ina ya thambo ndi kuzungulira mpaka mbali inanso; palibe chinthu chotha kupewa kutentha kwake.
7 Lamulo la Yehova ndi langwiro, kutsitsimutsa moyo. Maumboni a Yehova ndi odalirika, amapereka nzeru kwa wopanda nzeru.
8 Malangizo a Yehova ndi olungama, amapereka chimwemwe mu mtima. Malamulo a Yehova ndi onyezimira, amapereka kuwala.
9 Kuopa Yehova ndiye chinthu changwiro, chimakhala mpaka muyaya. Maweruzo a Yehova ndi owona ndipo onse ndi olungama;
10 ndi a mtengowapatali kuposa golide, kuposa golide weniweni; ndi otsekemera kuposa uchi, kuposa uchi wochokera pa chisa chake.
11 Mtumiki wanu amachenjezedwa nawo; powasunga pali mphotho yayikulu.
12 Ndani angathe kudziwa zolakwa zake? Mundikhululukire zolakwa zanga zobisika.
13 Muteteze mtumiki wanunso ku machimo ochita akudziwa; iwo asandilamulire. Kotero ndidzakhala wosalakwa, wopanda mlandu wa tchimo lalikulu.
14 Mawu a mʼkamwa mwanga ndi zolingalira za mu mtima mwanga zikhale zokondweretsa pamaso panu, Inu Yehova, Thanthwe langa ndi Mpulumutsi wanga.