< Masalimo 17 >
1 Pemphero la Davide. Imvani Inu Yehova pempho langa lachilungamo; mverani kulira kwanga. Tcherani khutu kuti mumve pemphero langa popeza silikuchokera pakamwa pachinyengo.
大卫的祈祷。 耶和华啊,求你听闻公义, 侧耳听我的呼吁! 求你留心听我这不出于诡诈嘴唇的祈祷!
2 Kusalakwa kwanga kuchokera kwa inu; maso anu aone chimene ndi cholungama.
愿我的判语从你面前发出; 愿你的眼睛观看公正。
3 Ngakhale Inu mutafufuza mtima wanga ndi kundisanthula usiku, ngakhale mutandiyesa, simudzapeza kanthu; Ine ndatsimikiza kuti pakamwa panga sipadzachimwa.
你已经试验我的心; 你在夜间鉴察我; 你熬炼我,却找不着什么; 我立志叫我口中没有过失。
4 Kunena za ntchito za anthu, monga mwa mawu a pakamwa panu, Ine ndadzisunga ndekha posatsata njira zachiwawa.
论到人的行为,我借着你嘴唇的言语自己谨守, 不行强暴人的道路。
5 Mayendedwe anga akhazikika pa njira zanu; mapazi anga sanaterereke.
我的脚踏定了你的路径; 我的两脚未曾滑跌。
6 Ine ndikuyitana Inu, Mulungu wanga, pakuti mudzandiyankha; tcherani khutu lanu kwa ine ndipo mumve pemphero langa.
神啊,我曾求告你,因为你必应允我; 求你向我侧耳,听我的言语。
7 Onetsani kudabwitsa kwa chikondi chanu chachikulu, Inu amene mumapulumutsa ndi dzanja lanu lamanja iwo amene amathawira kwa inu kuchoka kwa adani awo.
求你显出你奇妙的慈爱来; 你是那用右手拯救投靠你的脱离起来攻击他们的人。
8 Mundisunge ine ngati mwanadiso; mundibise mu mthunzi wa mapiko anu,
求你保护我,如同保护眼中的瞳人; 将我隐藏在你翅膀的荫下,
9 kuchoka kwa oyipa amene amandizinga ine, kuchoka kwa anthu amene ndi adani anga, amene andizungulira ine.
使我脱离那欺压我的恶人, 就是围困我要害我命的仇敌。
10 Iwo amatseka mitima yawo yopanda chifundo, ndi pakamwa pawo amayankhula modzitamandira.
他们的心被脂油包裹; 他们用口说骄傲的话。
11 Andisaka, tsopano andizungulira ndi maso awo atcheru, kuti andigwetse pansi.
他们围困了我们的脚步; 他们瞪着眼,要把我们推倒在地。
12 Iwo ali ngati mkango wofuna nyama; ngati mkango waukulu wokhala mobisala.
他像狮子急要抓食, 又像少壮狮子蹲伏在暗处。
13 Dzukani Yehova, mulimbane nawo ndipo muwagwetse pansi; landitseni kuchoka kwa oyipa ndi lupanga lanu.
耶和华啊,求你起来,前去迎敌,将他打倒! 用你的刀救护我命脱离恶人。
14 Inu Yehova, pulumutseni ndi dzanja lanu kwa anthu otere, kwa anthu a dziko lino amene mphotho yawo ili mʼmoyo uno. Inu mumaletsa njala kwa amene asangalatsidwa nanu; ana awo aamuna ali ndi zinthu zambiri, ndipo iwo amasunga chuma cha ana awo.
耶和华啊,求你用手救我脱离世人, 脱离那只在今生有福分的世人! 你把你的财宝充满他们的肚腹; 他们因有儿女就心满意足, 将其余的财物留给他们的婴孩。
15 Ndipo ine mʼchilungamo ndidzaona nkhope yanu; pamene ndidzadzuka, ndidzakondwera kwambiri poonana nanu.
至于我,我必在义中见你的面; 我醒了的时候,得见你的形象就心满意足了。