< Masalimo 15 >
1 Salimo la Davide. Yehova, ndani angathe kukhala mʼmalo anu opatulika? Kodi ndani angathe kukhala mʼphiri lanu loyera?
Псало́м Давидів.
2 Munthu wa makhalidwe abwino, amene amachita zolungama, woyankhula choonadi chochokera mu mtima mwake,
Той, хто в невинності ходить, і праведність чинить, і правду говорить у серці своїм,
3 ndipo mʼkamwa mwake simutuluka mawu osinjirira, amene sachitira choyipa mnansi wake kapena kufalitsa mbiri yoyipa ya munthu mnzake,
хто не обмовля́є своїм язиком, і злого не чинить для друга свого, і свого ближнього не зневажає!
4 amene sapereka ulemu kwa munthu woyipa. Koma amalemekeza amene amaopa Yehova, amene amakwaniritsa zomwe walonjeza ngakhale pamene zikumupweteka,
Обридли́вий погорджений в очах його, і він богобі́йних шанує, присягає, для себе хоча б і на зло, — і дотримує;
5 amene amakongoletsa ndalama zake popanda chiwongoladzanja ndipo salandira chiphuphu pofuna kutsutsa anthu osalakwa. Iye amene amachita zinthu zimenezi sadzagwedezeka konse.
не дає свого срі́бла на ли́хву, і не бере на невинного пі́дкупу. Хто чинить таке, — ніко́ли той не захита́ється!