< Masalimo 147 >
1 Tamandani Yehova. Nʼkwabwino kwambiri kuyimba nyimbo zamatamando kwa Mulungu wathu, nʼkokondweretsa ndi koyenera kumutamanda!
你们要赞美耶和华! 因歌颂我们的 神为善为美; 赞美的话是合宜的。
2 Yehova akumanga Yerusalemu; Iye akusonkhanitsa amʼndende a Israeli.
耶和华建造耶路撒冷, 聚集以色列中被赶散的人。
3 Akutsogolera anthu osweka mtima ndi kumanga mabala awo.
他医好伤心的人, 裹好他们的伤处。
4 Amadziwa chiwerengero cha nyenyezi, ndipo iliyonse amayitchula dzina.
他数点星宿的数目, 一一称它的名。
5 Yehova ndi wamkulu ndi wamphamvu kwambiri; nzeru zake zilibe malire.
我们的主为大,最有能力; 他的智慧无法测度。
6 Yehova amagwiriziza anthu odzichepetsa, koma amagwetsa pansi anthu oyipa.
耶和华扶持谦卑人, 将恶人倾覆于地。
7 Imbirani Yehova ndi mayamiko; imbani nyimbo kwa Mulungu ndi pangwe.
你们要以感谢向耶和华歌唱, 用琴向我们的 神歌颂。
8 Iye amaphimba mlengalenga ndi mitambo; amapereka mvula ku dziko lapansi ndi kumeretsa udzu mʼmapiri.
他用云遮天,为地降雨, 使草生长在山上。
9 Iye amapereka chakudya kwa ngʼombe ndi kwa ana a makwangwala pamene akulira chakudya.
他赐食给走兽 和啼叫的小乌鸦。
10 Chikondwerero chake sichili mʼmphamvu za kavalo, kapena mʼmiyendo ya anthu amphamvu.
他不喜悦马的力大, 不喜爱人的腿快。
11 Yehova amakondwera ndi amene amamuopa, amene chiyembekezo chawo chili mʼchikondi chake chosasinthika.
耶和华喜爱敬畏他 和盼望他慈爱的人。
12 Lemekeza Yehova, iwe Yerusalemu; tamanda Mulungu wako, iwe Ziyoni,
耶路撒冷啊,你要颂赞耶和华! 锡安哪,你要赞美你的 神!
13 pakuti Iye amalimbitsa mipiringidzo ya zipata zako ndi kudalitsa anthu ako mwa iwe.
因为他坚固了你的门闩, 赐福给你中间的儿女。
14 Iye amabweretsa mtendere mʼmalire mwako ndi kukukhutitsa ndi ufa wa tirigu wosalala.
他使你境内平安, 用上好的麦子使你满足。
15 Iyeyo amapereka lamulo pa dziko lapansi; mawu ake amayenda mwaliwiro.
他发命在地; 他的话颁行最快。
16 Amagwetsa chisanu ngati ubweya ndi kumwaza chipale ngati phulusa.
他降雪如羊毛, 撒霜如炉灰。
17 Amagwetsa matalala ngati miyala. Kodi ndani angathe kupirira kuzizira kwake?
他掷下冰雹如碎渣; 他发出寒冷,谁能当得起呢?
18 Amatumiza mawu ake ndipo chisanucho chimasungunuka; amawombetsa mphepo ndipo madzi amayenda.
他一出令,这些就都消化; 他使风刮起,水便流动。
19 Iye anawulula mawu ake kwa Yakobo, malamulo ake ndi zophunzitsa zake kwa Israeli.
他将他的道指示雅各, 将他的律例典章指示以色列。
20 Sanachitepo zimenezi kwa mtundu wina uliwonse wa anthu; anthu enawo sadziwa malamulo ake. Tamandani Yehova.
别国他都没有这样待过; 至于他的典章,他们向来没有知道。 你们要赞美耶和华!