< Masalimo 145 >

1 Salimo la matamando la Davide. Ndidzakukwezani Mulungu wanga, Mfumu yanga; ndidzatamanda dzina lanu ku nthawi za nthawi.
תהלה לדוד ארוממך אלוהי המלך ואברכה שמך לעולם ועד
2 Ndidzakutamandani tsiku ndi tsiku ndi kulemekeza dzina lanu ku nthawi za nthawi.
בכל-יום אברכך ואהללה שמך לעולם ועד
3 Yehova ndi wamkulu ndi woyenera matamando onse; ukulu wake palibe angawumvetsetse.
גדול יהוה ומהלל מאד ולגדלתו אין חקר
4 Mʼbado wina udzayamikira ntchito yanu kwa mʼbado wina; Iwo adzafotokoza za machitidwe anu amphamvu.
דור לדור ישבח מעשיך וגבורתיך יגידו
5 Adzayankhula ulemerero wokongola waufumu wanu, ndipo ine ndidzalingalira za ntchito zanu zodabwitsa.
הדר כבוד הודך-- ודברי נפלאתיך אשיחה
6 Iwo adzafotokoza za mphamvu ya ntchito zanu zoopsa kwambiri, ndipo ine ndidzalengeza za ntchito zanu zazikulu.
ועזוז נוראתיך יאמרו וגדלותיך (וגדלתך) אספרנה
7 Adzakondwerera kuchuluka kwa ubwino wanu, ndi kuyimba mwachimwemwe za chilungamo chanu.
זכר רב-טובך יביעו וצדקתך ירננו
8 Yehova ndi wokoma mtima ndi wachifundo, wosakwiya msanga ndi wodzaza ndi chikondi chosasinthika.
חנון ורחום יהוה ארך אפים וגדל-חסד
9 Yehova ndi wabwino kwa onse; amachitira chifundo zonse zimene anazipanga.
טוב-יהוה לכל ורחמיו על-כל-מעשיו
10 Zonse zimene munazipanga zidzakutamandani, Inu Yehova; oyera mtima adzakulemekezani.
יודוך יהוה כל-מעשיך וחסידיך יברכוכה
11 Iwo adzafotokoza za ulemerero wa ufumu wanu ndi kuyankhula za mphamvu yanu,
כבוד מלכותך יאמרו וגבורתך ידברו
12 kuti anthu onse adziwe za machitidwe anu amphamvu ndi ulemerero wokongola wa ufumu wanu.
להודיע לבני האדם--גבורתיו וכבוד הדר מלכותו
13 Ufumu wanu ndi ufumu wamuyaya, ndipo ulamuliro wanu ndi wosatha pa mibado yonse. Yehova ndi wokhulupirika pa malonjezo ake onse ndi wokonda zonse zimene Iye anazipanga.
מלכותך מלכות כל-עלמים וממשלתך בכל-דור ודר
14 Yehova amagwiriziza onse amene akugwa ndipo amakweza onse otsitsidwa.
סומך יהוה לכל-הנפלים וזוקף לכל-הכפופים
15 Maso a onse amayangʼana kwa Inu, ndipo Inu mumawapatsa chakudya chawo pa nthawi yoyenera.
עיני-כל אליך ישברו ואתה נותן-להם את-אכלם בעתו
16 Mumatsekula dzanja lanu ndi kukwaniritsa zokhumba za chamoyo chilichonse.
פותח את-ידך ומשביע לכל-חי רצון
17 Yehova ndi wolungama mʼnjira zake zonse, ndi wokonda zonse zimene anazipanga.
צדיק יהוה בכל-דרכיו וחסיד בכל-מעשיו
18 Yehova ali pafupi ndi onse amene amamuyitana, onse amene amamuyitana Iye mʼchoonadi.
קרוב יהוה לכל-קראיו-- לכל אשר יקראהו באמת
19 Iye amakwaniritsa zokhumba za iwo amene amamuopa; amamva kulira kwawo ndi kuwapulumutsa.
רצון-יראיו יעשה ואת-שועתם ישמע ויושיעם
20 Yehova amayangʼana onse amene amamukonda koma adzawononga anthu onse oyipa.
שומר יהוה את-כל-אהביו ואת כל-הרשעים ישמיד
21 Pakamwa panga padzayankhula zotamanda Yehova. Cholengedwa chilichonse chitamande dzina lake loyera ku nthawi za nthawi.
תהלת יהוה ידבר-פי ויברך כל-בשר שם קדשו--לעולם ועד

< Masalimo 145 >