< Masalimo 143 >

1 Salimo la Davide. Yehova imvani pemphero langa, mvetserani kulira kwanga kopempha chifundo; mwa kukhulupirika kwanu ndi chilungamo chanu bwerani kudzandithandiza.
מִזְמוֹר לְדָוִד יְהוָה ׀ שְׁמַע תְּפִלָּתִי הַאֲזִינָה אֶל־תַּחֲנוּנַי בֶּאֱמֻנָתְךָ עֲנֵנִי בְּצִדְקָתֶֽךָ׃
2 Musazenge mlandu mtumiki wanu, pakuti palibe munthu wamoyo amene ndi wolungama pamaso panu.
וְאַל־תָּבוֹא בְמִשְׁפָּט אֶת־עַבְדֶּךָ כִּי לֹֽא־יִצְדַּק לְפָנֶיךָ כָל־חָֽי׃
3 Mdani akundithamangitsa, iye wandipondereza pansi; wachititsa kuti ndikhale mu mdima ngati munthu amene anafa kale.
כִּי רָדַף אוֹיֵב ׀ נַפְשִׁי דִּכָּא לָאָרֶץ חַיָּתִי הוֹשִׁיבַנִי בְמַחֲשַׁכִּים כְּמֵתֵי עוֹלָֽם׃
4 Choncho mzimu wanga ukufowoka mʼkati mwanga; mʼkati mwanga, mtima wanga uli ndi nkhawa.
וַתִּתְעַטֵּף עָלַי רוּחִי בְּתוֹכִי יִשְׁתּוֹמֵם לִבִּֽי׃
5 Ndimakumbukira masiku amakedzana; ndimalingalira za ntchito yanu yonse, ndimaganizira zimene manja anu anachita.
זָכַרְתִּי יָמִים ׀ מִקֶּדֶם הָגִיתִי בְכָל־פָּעֳלֶךָ בְּֽמַעֲשֵׂה יָדֶיךָ אֲשׂוֹחֵֽחַ׃
6 Ndatambalitsa manja anga kwa Inu; moyo wanga uli ndi ludzu lofuna Inu monga nthaka yowuma. (Sela)
פֵּרַשְׂתִּי יָדַי אֵלֶיךָ נַפְשִׁי ׀ כְּאֶֽרֶץ־עֲיֵפָה לְךָ סֶֽלָה׃
7 Yehova ndiyankheni msanga; mzimu wanga ukufowoka. Musandibisire nkhope yanu, mwina ndidzakhala ngati iwo amene atsikira ku dzenje.
מַהֵר עֲנֵנִי ׀ יְהוָה כָּלְתָה רוּחִי אַל־תַּסְתֵּר פָּנֶיךָ מִמֶּנִּי וְנִמְשַׁלְתִּי עִם־יֹרְדֵי בֽוֹר׃
8 Lolani kuti mmawa ubweretse mawu achikondi chanu chosasinthika, pakuti ine ndimadalira Inu. Mundisonyeze njira yoti ndiyendemo, pakuti kwa Inu nditukulira moyo wanga.
הַשְׁמִיעֵנִי בַבֹּקֶר ׀ חַסְדֶּךָ כִּֽי־בְךָ בָטָחְתִּי הוֹדִיעֵנִי דֶּֽרֶךְ־זוּ אֵלֵךְ כִּֽי־אֵלֶיךָ נָשָׂאתִי נַפְשִֽׁי׃
9 Pulumutseni kwa adani anga, Inu Yehova, pakuti ndimabisala mwa Inu.
הַצִּילֵנִי מֵאֹיְבַי ׀ יְהוָה אֵלֶיךָ כִסִּֽתִי׃
10 Phunzitseni kuchita chifuniro chanu, popeza ndinu Mulungu wanga; Mzimu wanu wabwino unditsogolere pa njira yanu yosalala.
לַמְּדֵנִי ׀ לַֽעֲשׂוֹת רְצוֹנֶךָ כִּֽי־אַתָּה אֱלוֹהָי רוּחֲךָ טוֹבָה תַּנְחֵנִי בְּאֶרֶץ מִישֽׁוֹר׃
11 Sungani moyo wanga Inu Yehova chifukwa cha dzina lanu; mwa chilungamo chanu tulutseni mʼmasautso anga.
לְמַֽעַן־שִׁמְךָ יְהוָה תְּחַיֵּנִי בְּצִדְקָתְךָ ׀ תּוֹצִיא מִצָּרָה נַפְשִֽׁי׃
12 Mwa chikondi chanu chosasinthika khalitsani chete adani anga; wonongani adani anga, pakuti ndine mtumiki wanu.
וּֽבְחַסְדְּךָ תַּצְמִית אֹיְבָי וְֽהַאֲבַדְתָּ כָּל־צֹרֲרֵי נַפְשִׁי כִּי אֲנִי עַבְדֶּֽךָ׃

< Masalimo 143 >