< Masalimo 141 >
1 Salimo la Davide. Inu Yehova ndikukuyitanani; bwerani msanga kwa ine. Imvani mawu anga pamene ndiyitana Inu.
YHWH, I cry unto thee: make haste unto me; give ear unto my voice, when I cry unto thee.
2 Pemphero langa lifike kwa Inu ngati lubani; kukweza manja kwanga kukhale ngati nsembe yamadzulo.
Let my prayer be set forth before thee as incense; and the lifting up of my hands as the evening sacrifice.
3 Yehova ikani mlonda pakamwa panga; londerani khomo la pa milomo yanga.
Set a watch, O YHWH, before my mouth; keep the door of my lips.
4 Musalole kuti mtima wanga ukokedwere ku zoyipa; kuchita ntchito zonyansa pamodzi ndi anthu amene amachita zoyipa; musalole kuti ndidye nawo zokoma zawo.
Incline not my heart to any evil thing, to practise wicked works with men that work iniquity: and let me not eat of their dainties.
5 Munthu wolungama andikanthe, chimenecho ndiye chifundo; andidzudzule ndiye mafuta pa mutu wanga. Mutu wanga sudzakana zimenezi. Komabe pemphero langa nthawi zonse ndi lotsutsana ndi ntchito za anthu ochita zoyipa.
Let the righteous smite me; it shall be a kindness: and let him reprove me; it shall be an excellent oil, which shall not break my head: for yet my prayer also shall be in their calamities.
6 Olamulira awo adzaponyedwa pansi kuchokera pa malo okwera kwambiri, ndipo anthu oyipa adzaphunzira kuti mawu anga anayankhulidwa bwino.
When their judges are overthrown in stony places, they shall hear my words; for they are sweet.
7 Iwo adzati, “Monga momwe nkhuni zimamwazikira akaziwaza, ndi momwenso mafupa athu amwazikira pa khomo la manda.” (Sheol )
Our bones are scattered at the grave's mouth, as when one cutteth and cleaveth wood upon the earth. (Sheol )
8 Koma maso anga akupenyetsetsa Inu Ambuye Wamphamvuzonse; ndimathawira kwa Inu, musandipereke ku imfa.
But mine eyes are unto thee, O Elohim YHWH: in thee is my trust; leave not my soul destitute.
9 Mundipulumutse ku misampha imene anditchera, ku makhwekhwe amene anthu oyipa andikonzera.
Keep me from the snares which they have laid for me, and the gins of the workers of iniquity.
10 Anthu oyipa akodwe mʼmaukonde awo, mpaka ine nditadutsa mwamtendere.
Let the wicked fall into their own nets, whilst that I withal escape.