< Masalimo 140 >
1 Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Landitseni Yehova kwa anthu oyipa; tetezeni kwa anthu ankhanza,
Al maestro del coro. Salmo. Di Davide. Salvami, Signore, dal malvagio, proteggimi dall'uomo violento,
2 amene mu mtima mwawo amakonza zinthu zoyipa ndi kuyambitsa nkhondo tsiku lililonse.
da quelli che tramano sventure nel cuore e ogni giorno scatenano guerre.
3 Iwo amanola malilime awo kukhala akuthwa ngati a njoka; pa milomo yawo pali ululu wa mamba. (Sela)
Aguzzano la lingua come serpenti; veleno d'aspide è sotto le loro labbra.
4 Tetezeni Inu Yehova, kwa anthu oyipa; tchinjirizeni kwa anthu ankhanza amene amakonza zokola mapazi anga.
Proteggimi, Signore, dalle mani degli empi, salvami dall'uomo violento: essi tramano per farmi cadere.
5 Anthu odzikuza anditchera msampha mobisika; iwo atchera zingwe za maukonde awo ndipo anditchera misampha pa njira yanga. (Sela)
I superbi mi tendono lacci e stendono funi come una rete, pongono agguati sul mio cammino.
6 Inu Yehova, ine ndikuti, “Ndinu Mulungu wanga.” Imvani kupempha kwanga Yehova.
Io dico al Signore: «Tu sei il mio Dio; ascolta, Signore, la voce della mia preghiera».
7 Inu Ambuye Wamphamvuzonse, Mpulumutsi wanga wamphamvu, mumateteza mutu wanga tsiku lankhondo.
Signore, mio Dio, forza della mia salvezza, proteggi il mio capo nel giorno della lotta.
8 Musawapatse anthu oyipa zokhumba zawo, Inu Yehova; musalole kuti zokonza zawo zitheke, mwina iwo adzayamba kunyada. (Sela)
Signore, non soddisfare i desideri degli empi, non favorire le loro trame.
9 Mitu ya amene andizungulira iphimbidwe ndi masautso amene milomo yawo yayambitsa.
Alzano la testa quelli che mi circondano, ma la malizia delle loro labbra li sommerge.
10 Makala amoto agwere pa iwo; aponyedwe pa moto, mʼmaenje amatope, asatulukemonso.
Fà piovere su di loro carboni ardenti, gettali nel bàratro e più non si rialzino.
11 Musalole kuti anthu achipongwe akhazikike mʼdziko; choyipa chilondole anthu ankhanza.
Il maldicente non duri sulla terra, il male spinga il violento alla rovina.
12 Ndikudziwa kuti Yehova amapereka chiweruzo cholungama kwa anthu osauka, ndipo amateteza zolinga za anthu osowa.
So che il Signore difende la causa dei miseri, il diritto dei poveri.
13 Zoonadi anthu olungama adzatamanda dzina lanu, ndipo anthu owongoka mtima adzakhala pamaso panu.
Sì, i giusti loderanno il tuo nome, i retti abiteranno alla tua presenza.