< Masalimo 139 >

1 Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Inu Yehova, mwandisanthula ndipo mukundidziwa.
למנצח לדוד מזמור יהוה חקרתני ותדע
2 Inu mumadziwa pamene ndikhala pansi ndi pamene ndidzuka; mumazindikira maganizo anga muli kutali.
אתה ידעת שבתי וקומי בנתה לרעי מרחוק
3 Mumapenyetsetsa pamene ndikutuluka ndi kugona kwanga; mumadziwa njira zanga zonse.
ארחי ורבעי זרית וכל-דרכי הסכנתה
4 Mawu asanatuluke pa lilime langa mumawadziwa bwinobwino, Inu Yehova.
כי אין מלה בלשוני הן יהוה ידעת כלה
5 Mumandizinga kumbuyo ndi kutsogolo komwe; mwasanjika dzanja lanu pa ine.
אחור וקדם צרתני ותשת עלי כפכה
6 Nzeru zimenezi ndi zopitirira nzeru zanga, ndi zapamwamba kuti ine ndizipeze.
פלאיה (פליאה) דעת ממני נשגבה לא-אוכל לה
7 Kodi ndingapite kuti kufuna kuzemba Mzimu wanu? Kodi ndingathawire kuti kuchoka pamaso panu?
אנה אלך מרוחך ואנה מפניך אברח
8 Ndikakwera kumwamba, Inu muli komweko; ndikakagona ku malo a anthu akufa, Inu muli komweko. (Sheol h7585)
אם אסק שמים שם אתה ואציעה שאול הנך (Sheol h7585)
9 Ngati ndiwulukira kotulukira dzuwa, ngati ndikakhala ku malekezero a nyanja,
אשא כנפי-שחר אשכנה באחרית ים
10 kumenekonso dzanja lanu lidzanditsogolera, dzanja lanu lamanja lidzandigwiriziza.
גם-שם ידך תנחני ותאחזני ימינך
11 Ndikanena kuti, “Zoonadi, mdima udzandibisa ndithu ndipo kuwunika kukhale mdima mondizungulira,”
ואמר אך-חשך ישופני ולילה אור בעדני
12 komabe mdimawo sudzakhala mdima kwa Inu; usiku udzawala ngati masana, pakuti mdima uli ngati kuwunika kwa Inu.
גם-חשך לא-יחשיך ממך ולילה כיום יאיר-- כחשיכה כאורה
13 Pakuti Inu munalenga za mʼkati mwanga; munandiwumba pamodzi mʼmimba mwa amayi anga.
כי-אתה קנית כליתי תסכני בבטן אמי
14 Ndimakuyamikani chifukwa ndinapangidwa mochititsa mantha ndi modabwitsa; ntchito zanu ndi zodabwitsa, zimenezi ndimazidziwa bwino lomwe.
אודך-- על כי נוראות נפליתי נפלאים מעשיך ונפשי ידעת מאד
15 Mapangidwe anga sanabisike pamaso panu pamene ndimapangidwa mʼmalo achinsinsi, pamene ndinkawumbidwa mwaluso mʼmimba ya amayi anga.
לא-נכחד עצמי ממך אשר-עשיתי בסתר רקמתי בתחתיות ארץ
16 Maso anu anaona thupi langa lisanawumbidwe. Masiku onse amene anapatsidwa kwa ine, analembedwa mʼbuku lanu asanayambe nʼkuwerengedwa komwe.
גלמי ראו עיניך ועל-ספרך כלם יכתבו ימים יצרו ולא (ולו) אחד בהם
17 Zolingalira zanu pa ine ndi zamtengowapatali, Inu Mulungu, ndi zosawerengeka ndithu!
ולי--מה-יקרו רעיך אל מה עצמו ראשיהם
18 Ndikanaziwerenga, zikanakhala zochuluka kuposa mchenga; pamene ndadzuka, ndili nanube.
אספרם מחול ירבון הקיצתי ועודי עמך
19 Ndi bwino mukanangopha anthu oyipa, Inu Mulungu! Chokereni inu anthu owononga anzanu!
אם-תקטל אלוה רשע ואנשי דמים סורו מני
20 Amayankhula za Inu ndi zolinga zoyipa; adani anu amagwiritsa ntchito dzina lanu molakwika.
אשר ימרוך למזמה נשוא לשוא עריך
21 Kodi ine sindidana nawo amene amakudani, Inu Yehova? Kodi sindinyansidwa nawo amene amakuwukirani?
הלוא-משנאיך יהוה אשנא ובתקוממיך אתקוטט
22 Ndimadana nawo kwathunthu; ndi adani anga.
תכלית שנאה שנאתים לאויבים היו לי
23 Santhuleni, Inu Mulungu ndipo mudziwe mtima wanga; Yeseni ndipo mudziwe zolingalira zanga.
חקרני אל ודע לבבי בחנני ודע שרעפי
24 Onani ngati muli mayendedwe aliwonse oyipa mwa ine, ndipo munditsogolere mʼnjira yanu yamuyaya.
וראה אם-דרך-עצב בי ונחני בדרך עולם

< Masalimo 139 >