< Masalimo 137 >
1 Mʼmbali mwa mitsinje ya ku Babuloni tinakhala pansi ndi kulira pamene tinakumbukira Ziyoni.
By the waters of Babylon there we sat, and we wept at the thought of Zion.
2 Kumeneko, pa mitengo ya misondozi tinapachika apangwe athu,
There on the poplars we hung our harps.
3 pakuti anthu otigwira ukapolo anatipempha kuti tiyimbe nyimbo. Otizunza athu anafuna nyimbo zachisangalalo; iwo anati, “Tiyimbireni imodzi mwa nyimbo za ku Ziyoni!”
For there our captors called for a song: our tormentors, rejoicing, saying: ‘Sing us one of the songs of Zion.’
4 Tingayimbe bwanji nyimbo za Yehova mʼdziko lachilendo?
How can we sing the Lord’s song in the foreigner’s land?
5 Ndikakuyiwala iwe Yerusalemu, dzanja langa lamanja liyiwale luso lake.
If I forget you, Jerusalem, may my right hand wither.
6 Lilime langa limamatire ku nkhama za mʼkamwa mwanga ndikapanda kukukumbukira iwe Yerusalemu, ngati sindiyesa iwe chimwemwe changa chachikulu.
May my tongue stick to the roof of my mouth, if I am unmindful of you, or don’t set Jerusalem above my chief joy.
7 Kumbukirani, Inu Yehova, zimene Aedomu anachita pa tsiku limene Yerusalemu anagonja. Iwowo anafuwula kuti, “Mugwetseni pansi, mugwetseni pansi mpaka pa maziko ake!”
Remember the Edomites, Lord, the day of Jerusalem’s fall, when they said, ‘Lay her bare, lay her bare, right down to her very foundation.’
8 Iwe mwana wa mkazi wa Babuloni, woyenera kuwonongedwa, wodalitsika ndi yemwe adzakubwezera pa zimene watichitira.
Babylon, despoiler, happy are those who pay you back for all you have done to us.
9 Amene adzagwira makanda ako ndi kuwakankhanthitsa pa miyala.
Happy are they who seize and dash your children against the rocks.