< Masalimo 134 >

1 Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. Bwerani, mutamande Yehova, inu atumiki onse a Yehova, amene mumatumikira usiku mʼnyumba ya Yehova.
Wimbo wa kwenda juu. Msifuni Bwana, ninyi nyote watumishi wa Bwana, ninyi mnaotumika usiku ndani ya nyumba ya Bwana.
2 Kwezani manja anu mʼmalo opatulika ndipo mutamande Yehova.
Inueni mikono yenu katika pale patakatifu na kumsifu Bwana.
3 Yehova wolenga kumwamba ndi dziko lapansi, akudalitseni kuchokera mʼZiyoni.
Naye Bwana, Muumba wa mbingu na dunia, awabariki kutoka Sayuni.

< Masalimo 134 >