< Masalimo 133 >
1 Salimo la Davide. Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. Onani, nʼkokoma ndi kokondweretsa ndithu pamene abale akhala pamodzi mwachiyanjano!
Píseň stupňů, Davidova. Aj, jak dobré a jak utěšené, když bratří v jednomyslnosti přebývají!
2 Zili ngati mafuta amtengowapatali othiridwa pa mutu, otsikira ku ndevu, ku ndevu za Aaroni, oyenderera mpaka mʼkhosi mwa mkanjo wake.
Jako mast výborná na hlavě, sstupující na bradu, bradu Aronovu, tekoucí až i na podolek roucha jeho.
3 Zili ngati mame a ku Heremoni otsikira pa Phiri la Ziyoni. Pakuti pamenepo Yehova amaperekapo dalitso, ndiwo moyo wamuyaya.
A jako rosa Hermon, kteráž sstupuje na hory Sionské. Nebo tu udílí Hospodin požehnání i života až na věky.