< Masalimo 130 >
1 Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. Ndikulirira kwa Inu Yehova ndili mʼdzenje lozama;
The song of greces. Lord, Y criede to thee fro depthes; Lord, here thou mi vois.
2 Ambuye imvani mawu anga. Makutu anu akhale tcheru kumva kupempha chifundo kwanga.
Thin eeris be maad ententif; in to the vois of my biseching.
3 Inu Yehova, mukanamawerengera machimo, Inu Yehova, akanayima chilili ndani wopanda mlandu?
Lord, if thou kepist wickidnessis; Lord, who schal susteyne?
4 Koma kwa Inu kuli chikhululukiro; nʼchifukwa chake mumaopedwa.
For merci is at thee; and, Lord, for thi lawe Y abood thee. Mi soule susteynede in his word; my soule hopide in the Lord.
5 Ndimayembekezera Yehova, moyo wanga umayembekezera, ndipo ndimakhulupirira mawu ake.
Fro the morewtid keping til to niyt;
6 Moyo wanga umayembekezera Ambuye, kupambana momwe alonda amayembekezera mmawa, inde, kupambana momwe alonda amayembekezera mmawa,
Israel hope in the Lord.
7 Yembekeza Yehova, iwe Israeli, pakuti Yehova ali ndi chikondi chosasinthika ndipo alinso ndi chipulumutso chochuluka.
For whi merci is at the Lord; and plenteous redempcioun is at hym.
8 Iye mwini adzawombola Israeli ku machimo ake onse.
And he schal ayen bie Israel; fro alle the wickidnessis therof.