< Masalimo 13 >
1 Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Mpaka liti Yehova? Kodi mudzandiyiwala mpaka kalekale? Mpaka liti mudzandibisira nkhope yanu?
For the choirmaster. A Psalm of David. How long, O LORD? Will You forget me forever? How long will You hide Your face from me?
2 Ndidzalimbana ndi maganizo anga ndi kukhala ndi chisoni mu mtima mwanga tsiku lililonse mpaka liti? Mpaka liti adani anga adzandipambana?
How long must I wrestle in my soul, with sorrow in my heart each day? How long will my enemy dominate me?
3 Ndiyangʼaneni ndi kundiyankha, Inu Yehova Mulungu wanga. Walitsani maso anga kuti ndingafe;
Consider me and respond, O LORD my God. Give light to my eyes, lest I sleep in death,
4 mdani wanga adzati, “Ndamugonjetsa,” ndipo adani anga adzakondwera pamene ine ndagwa.
lest my enemy say, “I have overcome him,” and my foes rejoice when I fall.
5 Koma ndikudalira chikondi chanu chosasinthika; mtima wanga umakondwera ndi chipulumutso chanu.
But I have trusted in Your loving devotion; my heart will rejoice in Your salvation.
6 Ine ndidzayimbira Yehova pakuti wandichitira zokoma.
I will sing to the LORD, for He has been good to me.