< Masalimo 128 >

1 Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. Odala ndi onse amene amaopa Yehova, amene amayenda mʼnjira zake.
(성전에 올라가는 노래) 여호와를 경외하며 그 도에 행하는 자마다 복이 있도다
2 Udzadya chipatso cha ntchito yako; madalitso ndi chuma zidzakhala zako.
네가 네 손이 수고한대로 먹을 것이라 네가 복되고 형통하리로다
3 Mkazi wako adzakhala ngati mpesa wobereka mʼkati mwa nyumba yako; ana ako adzakhala ngati mphukira za mitengo ya olivi kuzungulira tebulo lako.
네 집 내실에 있는 네 아내는 결실한 포도나무 같으며 네 상에 둘린 자식은 어린 감람나무 같으리로다
4 Ameneyu ndiye munthu wodalitsidwa amene amaopa Yehova.
여호와를 경외하는 자는 이같이 복을 얻으리로다
5 Yehova akudalitse kuchokera mʼZiyoni masiku onse a moyo wako; uwone zokoma za Yerusalemu,
여호와께서 시온에서 네게 복을 주실지어다 너는 평생에 예루살렘의 복을 보며
6 ndipo ukhale ndi moyo kuti udzaone zidzukulu zako. Mtendere ukhale ndi Israeli.
네 자식을 볼지어다 이스라엘에게 평강이 있을지로다

< Masalimo 128 >