< Masalimo 127 >
1 Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. Salimo la Solomoni. Yehova akapanda kumanga nyumba, omanga nyumbayo agwira ntchito pachabe. Yehova akapanda kulondera mzinda, mlonda akanangolondera pachabe.
솔로몬의 시 곧 성전에 올라가는 노래 여호와께서 집을 세우지 아니하시면 세우는 자의 수고가 헛되며 여호와께서 성을 지키지 아니하시면 파수꾼의 경성함이 허사로다
2 Mumangodzivuta nʼkulawirira mmamawa ndi kusagona msanga madzulo, kuvutikira chakudya choti mudye, pakuti Iye amapereka tulo kwa amene amawakonda.
너희가 일찍이 일어나고 늦게 누우며 수고의 떡을 먹음이 헛되도다 그러므로 여호와께서 그 사랑하시는 자에게는 잠을 주시는도다
3 Ana ndiye cholowa chochokera kwa Yehova, ana ndi mphotho yochokera kwa Iye.
자식은 여호와의 주신 기업이요 태의 열매는 그의 상급이로다
4 Ana a pa unyamata ali ngati mivi mʼmanja mwa munthu wankhondo.
젊은 자의 자식은 장사의 수중의 화살 같으니
5 Wodala munthu amene motengera mivi mwake mwadzaza. Iwo sadzachititsidwa manyazi pamene alimbana ndi adani awo pa zipata.
이것이 그 전통에 가득한 자는 복되도다 저희가 성문에서 그 원수와 말할 때에 수치를 당치 아니하리로다