< Masalimo 126 >
1 Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. Yehova atabwezera akapolo ku Ziyoni, tinali ngati amene akulota.
上行之詩。 當耶和華將那些被擄的帶回錫安的時候, 我們好像做夢的人。
2 Pakamwa pathu panadzaza ndi kuseka; malilime athu ndi nyimbo zachimwemwe. Pamenepo kunanenedwa pakati pa anthu kuti, “Yehova wawachitira zinthu zazikulu.”
我們滿口喜笑、 滿舌歡呼的時候, 外邦中就有人說: 耶和華為他們行了大事!
3 Yehova watichitira zinthu zazikulu, ndipo tadzazidwa ndi chimwemwe.
耶和華果然為我們行了大事, 我們就歡喜。
4 Tibwezereni madalitso athu, Inu Yehova, monga mitsinje ya ku Negevi.
耶和華啊,求你使我們被擄的人歸回, 好像南地的河水復流。
5 Iwo amene amafesa akulira, adzakolola akuyimba nyimbo zachimwemwe.
流淚撒種的, 必歡呼收割!
6 Iye amene amayendayenda nalira, atanyamula mbewu yokafesa, adzabwerera akuyimba nyimbo zachimwemwe, atanyamula mitolo yake.
那帶種流淚出去的, 必要歡歡樂樂地帶禾捆回來!