< Masalimo 125 >

1 Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. Amene amadalira Yehova ali ngati phiri la Ziyoni, limene silingagwedezeke koma ndi lokhala mpaka muyaya.
성전에 올라가는 노래 여호와를 의뢰하는 자는 시온 산이 요동치 아니하고 영원히 있음 같도다
2 Monga mapiri azungulira Yerusalemu, momwemonso Yehova azungulira anthu ake kuyambira tsopano mpaka muyaya.
산들이 예루살렘을 두름과 같이 여호와께서 그 백성을 지금부터 영원까지 두르시리로다
3 Ndodo yaufumu ya anthu oyipa sidzakhala pa dziko limene lapatsidwa kwa anthu olungama, kuti anthu olungamawo angachite nawonso zoyipa.
악인의 권세가 의인의 업에 미치지 못하리니 이는 의인으로 죄악에 손을 대지 않게 함이로다
4 Yehova chitirani zabwino amene ndi abwino, amene ndi olungama mtima
여호와여 선인에게와 마음이 정직한 자에게 선을 행하소서
5 Koma amene amatembenukira ku njira zokhotakhota, Yehova adzawachotsa pamodzi ndi anthu ochita zoyipa. Mtendere ukhale pa Israeli.
자기의 굽은 길로 치우치는 자를 여호와께서 죄악을 짓는 자와 함께 다니게 하시리로다 이스라엘에게는 평강이 있을지어다

< Masalimo 125 >