< Masalimo 123 >

1 Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. Ndikweza maso anga kwa Inu, kwa Inu amene mumakhala kumwamba.
שיר המעלות אליך נשאתי את-עיני-- הישבי בשמים
2 Taonani, monga momwe maso a akapolo amayangʼana mʼdzanja la mbuye wawo, monga momwenso maso a mdzakazi amayangʼana mʼdzanja la dona wake, choncho maso athu ali kwa Yehova Mulungu wathu, mpaka atichitire chifundo.
הנה כעיני עבדים אל-יד אדוניהם-- כעיני שפחה אל-יד גברתה כן עינינו אל-יהוה אלהינו-- עד שיחננו
3 Mutichitire chifundo, Inu Yehova mutichitire chifundo, pakuti tapirira chitonzo chachikulu.
חננו יהוה חננו כי-רב שבענו בוז
4 Ife tapirira mnyozo wambiri kuchokera kwa anthu odzikuza, chitonzo chachikulu kuchokera kwa anthu onyada.
רבת שבעה-לה נפשנו הלעג השאננים הבוז לגאיונים (לגאי יונים)

< Masalimo 123 >