< Masalimo 122 >

1 Salimo la Davide. Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. Ndinakondwera atandiwuza kuti, “Tiyeni ku nyumba ya Yehova.”
(Sang til Festrejserne. Af David.) Jeg frydede mig, da de sagde til mig: "Vi drager til HERRENs Hus!"
2 Mapazi athu akuyima mʼzipata zako, Iwe Yerusalemu.
Så står vore Fødder da i dine Porte, Jerusalem,
3 Yerusalemu anamangidwa ngati mzinda umene uli wothithikana pamodzi.
Jerusalem bygget som Staden, hvor Folket samles;
4 Kumeneko ndiye kumene kumapita mafuko, mafuko a Yehova, umboni wa kwa Israeli, kuti atamande dzina la Yehova.
thi did op drager Stammerne, HERRENs Stammer en Vedtægt for Israel om at prise HERRENs Navn.
5 Kumeneko anayikako mipando yaufumu yachiweruzo, mipando yaufumu ya nyumba ya Davide.
Thi der står Dommersæder, Sæder for Davids Hus.
6 Pemphererani mtendere wa Yerusalemu: “Iwo amene amakukonda iwe zinthu ziwayendere bwino.
Bed om Jerusalems Fred! Ro finde de, der elsker dig!
7 Mukhale mtendere mʼkati mwa makoma ako, ndipo mʼnyumba zako zaufumu mukhale chitetezo.”
Der råde Fred på din Mur, Tryghed i dine Borge!
8 Chifukwa cha abale anga ndi abwenzi anga ndidzati, “Mtendere ukhale mʼkati mwako.”
For Brødres og Frænders Skyld vil jeg ønske dig Fred,
9 Chifukwa cha Nyumba ya Yehova Mulungu wathu, ndidzakufunira zabwino.
for Herren vor Guds hus's skyld vil jeg søge dit bedste.

< Masalimo 122 >