< Masalimo 121 >
1 Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. Ndikweza maso anga ku mapiri; kodi thandizo langa limachokera kuti?
A Song of Ascents. I will lift up my eyes to the hills. Where does my help come from?
2 Thandizo langa limachokera kwa Yehova, wolenga kumwamba ndi dziko lapansi.
My help comes from the LORD, who made heaven and earth.
3 Sadzalola kuti phazi lako literereke; Iye amene amakusunga sadzawodzera.
He will not allow your foot to be moved. He who keeps you will not slumber.
4 Taonani, Iye amene amasunga Israeli sadzawodzera kapena kugona.
Behold, he who keeps Israel will neither slumber nor sleep.
5 Yehova ndiye amene amakusunga; Yehova ndiye mthunzi wako ku dzanja lako lamanja.
The LORD is your keeper. The LORD is your shade on your right hand.
6 Dzuwa silidzakupweteka nthawi ya masana, kapena mwezi nthawi ya usiku.
The sun will not harm you by day, nor the moon by night.
7 Yehova adzakuteteza ku zoyipa zonse; adzasunga moyo wako.
The LORD will keep you from all evil. He will keep your soul.
8 Yehova adzayangʼanira kutuluka kwako ndi kulowa kwako; kuyambira tsopano mpaka muyaya.
The LORD will keep your going out and your coming in, from this time forward, and forever more.