< Masalimo 120 >

1 Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. Ndimafuwulira kwa Yehova mʼmasautso anga, ndipo Iye amandiyankha.
都もうでの歌 わたしが悩みのうちに、主に呼ばわると、主はわたしに答えられる。
2 Pulumutseni Yehova ku milomo yabodza, ndi kwa anthu achinyengo.
「主よ、偽りのくちびるから、欺きの舌から、わたしを助け出してください」。
3 Kodi adzakuchitani chiyani, ndipo adzawonjezerapo zotani, inu anthu achinyengo?
欺きの舌よ、おまえに何が与えられ、何が加えられるであろうか。
4 Adzakulangani ndi mivi yakuthwa ya munthu wankhondo, ndi makala oyaka a mtengo wa tsanya.
ますらおの鋭い矢と、えにしだの熱い炭とである。
5 Tsoka ine kuti ndimakhala ku Mesaki, kuti ndimakhala pakati pa matenti a ku Kedara!
わざわいなるかな、わたしはメセクにやどり、ケダルの天幕のなかに住んでいる。
6 Kwa nthawi yayitali ndakhala pakati pa iwo amene amadana ndi mtendere.
わたしは久しく平安を憎む者のなかに住んでいた。
7 Ine ndine munthu wamtendere; koma ndikamayankhula, iwo amafuna nkhondo.
わたしは平安を願う、しかし、わたしが物言うとき、彼らは戦いを好む。

< Masalimo 120 >