< Masalimo 118 >

1 Yamikani Yehova chifukwa ndi wabwino; pakuti chikondi chake chosasinthika ndi chosatha.
'O give thanks unto the LORD, for He is good, for His mercy endureth for ever.'
2 Israeli anene kuti: “Chikondi chake ndi chosatha.”
So let Israel now say, for His mercy endureth for ever,
3 Banja la Aaroni linene kuti, “Chikondi chake ndi chosatha.”
So let the house of Aaron now say, for His mercy endureth for ever.
4 Iwo amene amaopa Yehova anene kuti: “Chikondi chake ndi chosatha.”
So let them now that fear the LORD say, for His mercy endureth for ever.
5 Ndili mʼmasautso anga ndinalirira Yehova, ndipo Iye anayankha pondichotsa mʼmasautsowo.
Out of my straits I called upon the LORD; He answered me with great enlargement.
6 Yehova ali nane; sindidzachita mantha. Munthu angandichite chiyani?
The LORD is for me; I will not fear; what can man do unto me?
7 Yehova ali nane; Iye ndiye thandizo langa. Ndidzayangʼana adani anga mwachipambano.
The LORD is for me as my helper; and I shall gaze upon them that hate me.
8 Nʼkwabwino kuthawira kwa Yehova kusiyana ndi kudalira munthu.
It is better to take refuge in the LORD than to trust in man.
9 Nʼkwabwino kuthawira kwa Yehova kusiyana ndi kudalira mafumu.
It is better to take refuge in the LORD than to trust in princes.
10 Anthu a mitundu yonse anandizinga, koma mʼdzina la Yehova ndinawawononga.
All nations compass me about; verily, in the name of the LORD I will cut them off.
11 Anandizinga mbali zonse, koma mʼdzina la Yehova ndinawawononga.
They compass me about, yea, they compass me about; verily, in the name of the LORD I will cut them off.
12 Anandizinga ngati njuchi, koma anatha msanga ngati moto wapaminga; mʼdzina la Yehova ndinawawononga.
They compass me about like bees; they are quenched as the fire of thorns; verily, in the name of the LORD I will cut them off.
13 Anandikankha uku ndi uko ndipo ndinali pafupi kugwa, koma Yehova anandithandiza.
Thou didst thrust sore at me that I might fall; but the LORD helped me.
14 Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga; Iye wakhala chipulumutso changa.
The LORD is my strength and song; and He is become my salvation.
15 Mfuwu wachimwemwe ndi chipambano ukumveka mʼmatenti a anthu olungama mtima kuti: “Dzanja lamanja la Yehova lachita zamphamvu!
The voice of rejoicing and salvation is in the tents of the righteous; the right hand of the LORD doeth valiantly.
16 Dzanja lamanja la Yehova latukulidwa mmwamba Dzanja lamanja la Yehova lachita zamphamvu!”
The right hand of the LORD is exalted; the right hand of the LORD doeth valiantly.
17 Sindidzafa koma ndidzakhala ndi moyo ndipo ndidzalalika za ntchito ya Yehova.
I shall not die, but live, and declare the works of the LORD.
18 Yehova wandilanga koopsa, koma sanandipereke ku imfa.
The LORD hath chastened me sore; but He hath not given me over unto death.
19 Tsekulireni zipata zachilungamo, kuti ndifike kudzayamika Yehova.
Open to me the gates of righteousness; I will enter into them, I will give thanks unto the LORD.
20 Ichi ndicho chipata cha Yehova chimene olungama mtima okha adzalowerapo.
This is the gate of the LORD; the righteous shall enter into it.
21 Ndidzakuyamikani chifukwa Inu munandiyankha; mwakhala chipulumutso changa.
I will give thanks unto Thee, for Thou hast answered me, and art become my salvation.
22 Mwala umene amisiri omanga nyumba anawukana wasanduka wapangodya;
The stone which the builders rejected is become the chief corner-stone.
23 Yehova ndiye wachita zimenezi ndipo nʼzodabwitsa pamaso pathu.
This is the LORD'S doing; it is marvellous in our eyes.
24 Lero ndiye tsiku limene Yehova walipanga; tiyeni tikondwere ndi kusangalala nalo.
This is the day which the LORD hath made; we will rejoice and be glad in it.
25 Inu Yehova, tipulumutseni; Yehova, tipambanitseni.
We beseech Thee, O LORD, save now! We beseech Thee, O LORD, make us now to prosper!
26 Wodala amene akubwera mʼdzina la Yehova. Tikukudalitsani kuchokera ku nyumba ya Yehova.
Blessed be he that cometh in the name of the LORD; we bless you out of the house of the LORD.
27 Yehova ndi Mulungu, ndipo kuwala kwake kwatiwunikira Ife. Lowani nawo pa mʼdipiti wa ku chikondwerero mutanyamula nthambi mʼdzanja lanu, mpaka ku nyanga za guwa.
The LORD is God, and hath given us light; order the festival procession with boughs, even unto the horns of the altar.
28 Inu ndinu Mulungu wanga, ndipo ndidzakuyamikani; Inu ndinu Mulungu wanga, ndipo ndidzakukwezani.
Thou art my God, and I will give thanks unto Thee; Thou art my God, I will exalt Thee.
29 Yamikani Yehova chifukwa ndi wabwino; pakuti chikondi chake chosasinthika ndi chosatha.
O give thanks unto the LORD, for He is good, for His mercy endureth for ever.

< Masalimo 118 >