< Masalimo 116 >
1 Ndimakonda Yehova pakuti Iyeyo amamva mawu anga; Iye amamva kulira kwanga kopempha chifundo.
Minä rakastan Herraa, sillä hän kuulee minun ääneni ja rukoukseni;
2 Pakuti ananditchera khutu, ndidzayitana Iye masiku onse a moyo wanga.
sillä hän on kallistanut korvansa minun puoleeni, ja minä huudan häntä avuksi kaiken elinaikani.
3 Zingwe za imfa zinandizinga, zoopsa za ku dziko la anthu akufa zinandigwera; ndinapeza mavuto ndi chisoni. (Sheol )
Kuoleman paulat piirittivät minut, tuonelan ahdistukset kohtasivat minua; minä jouduin hätään ja murheeseen. (Sheol )
4 Pamenepo ndinayitana dzina la Yehova: “Inu Yehova, pulumutseni!”
Mutta minä huusin avukseni Herran nimeä: "Oi Herra, pelasta minun sieluni!"
5 Yehova ndi wokoma mtima ndi wolungama Mulungu wathu ndi wodzaza ndi chifundo.
Herra on armollinen ja vanhurskas, meidän Jumalamme on laupias.
6 Yehova amateteza munthu wodzichepetsa mtima; pamene ndinali ndi chosowa chachikulu, Iye anandipulumutsa.
Herra varjelee yksinkertaiset; minä olin viheliäinen, mutta hän auttoi minua.
7 Pumula iwe moyo wanga, pakuti Yehova wakuchitira zokoma.
Palaja, sieluni, takaisin lepoosi, sillä Herra on tehnyt sinulle hyvin.
8 Pakuti Inu Yehova mwapulumutsa moyo wanga ku imfa, maso anga ku misozi, mapazi anga kuti angapunthwe,
Sillä sinä olet pelastanut minun sieluni kuolemasta, minun silmäni kyynelistä, jalkani kompastumasta.
9 kuti ine ndiyende pamaso pa Yehova mʼdziko la anthu amoyo.
Minä saan vaeltaa Herran kasvojen edessä elävien maassa.
10 Ine ndinakhulupirira; choncho ndinati, “Ndasautsidwa kwambiri.”
Minä uskon, sentähden minä puhun, minä, joka olin kovin vaivattu.
11 Ndipo ndili mʼnkhawa yanga ndinati, “Anthu onse ndi abodza.”
Minä sanoin hädässäni: "Kaikki ihmiset ovat valhettelijoita".
12 Ndingamubwezere chiyani Yehova, chifukwa cha zokoma zake zonse zimene wandichitira?
Kuinka minä maksan Herralle kaikki hänen hyvät tekonsa minua kohtaan?
13 Ndidzakweza chikho cha chipulumutso ndipo ndidzayitana dzina la Yehova.
Minä kohotan pelastuksen maljan ja huudan avukseni Herran nimeä.
14 Ndidzakwaniritsa malonjezo anga kwa Yehova pamaso pa anthu ake onse.
Minä täytän lupaukseni Herralle kaiken hänen kansansa edessä.
15 Imfa ya anthu oyera mtima ndi yamtengowapatali pamaso pa Yehova.
Kallis on Herran silmissä hänen hurskaittensa kuolema.
16 Inu Yehova, zoonadi ndine mtumiki wanu: ndine mtumiki wanu, mwana wa mdzakazi wanu; Inu mwamasula maunyolo anga.
Oi Herra, minä olen sinun palvelijasi, sinun palvelijasi minä olen, sinun palvelijattaresi poika! Sinä päästit minun siteeni.
17 Ndidzapereka nsembe yachiyamiko kwa Inu ndipo ndidzayitanira pa dzina la Yehova.
Sinulle minä uhraan kiitosuhrin ja huudan avukseni Herran nimeä.
18 Ndidzakwaniritsa malonjezo anga kwa Yehova pamaso pa anthu ake onse,
Minä täytän lupaukseni Herralle kaiken hänen kansansa edessä
19 mʼmabwalo a nyumba ya Yehova, mʼkati mwako iwe Yerusalemu. Tamandani Yehova.
Herran huoneen esikartanoissa, sinun keskelläsi, Jerusalem. Halleluja!